Upload
hoangthien
View
215
Download
0
Embed Size (px)
Citation preview
Okondedwa CONTACT NAME
dzina langa ndine NAME ndimagwira ntchito ku Cultural Survival, bungwe lomwe limagwira ntchito ndi anthu pofuna kuteteza malo, awo, ziyankhulo zawo, zikhalidwe zawo komanso ufulu wawo. Ndikukumemani kuti mukhale nafe poteteza ufulu wa anthu.
Bungwe la Cultural Survival limakonza ma pologalamu aulere pa wayilesi padziko lonse pansi kuwadziwitsa anthu zoti ali ndi ufufu ochita zofuna zawo,ndikudziwitsidwa zinthu zinthu sizanachitike ngati magulu akunja akufuna kugwiritsa ntchito malo komanso zinthu zawo zisanagwiritsidwe ntchito.
Tsatirani ndondomeko ya mapologalamu a pa wayilesi apa: LINK SPECIFIC SETS
Uthenga wa mawu ulipo mu ziyankhulo zochepa koma tili ndi uthenga wolembedwa m’chichewa womwe waphatikizidwa. Ngati muli okondwa kuthandauzira mu chiyankhulo chomwe omvera anu angamve, tidzakodwa mutatitumiziranso mukathandauzira.
Tikudikilira yankho lanu. Chonde yakhani ngati nyumba yanu yowulutsira mawu ili yokondwa kugwira nafe ncthito kapena ngati muli ndi mafunso aliwonse.
Kuti mudziwe zambiri za bungwe la Cultural Survival, Chonde tipezeni pa:
www.culturalsurvival.org
Ndatha ine wanuNAME
1. kodi ufulu wochita zomwe mwafuna,komanso kudziwitsidwa zinthu zisanachitike nchani?
Oyankhula oyamba:
Kodi mukudziwa kuti ufulu,wochita zomwe mwafuna komanso kudziwitsidwa zinthu
zisanachitidwe nchani ?
Oyankhula wachiwiri:
Eya! Ndi ufulu oti boma likuyenera kutidziwitsa m’madera athu pa za migodi, zitsime za mafuta,
madzi ndi zitukuko zina ndi zina zomwe zingakhanzikitsidwe m’madera athu. Chinanso
n’chakuti boma likuyenera kutimvera ndi kulemekeza maganizo athu ndikugwirizana chimodzi
ncthitozo zisanayambidwe m’madera athuwa.
Okamba nkhani:
Kuti mudziwe zambiri pitani pa , cultural survival dot org slash consent[culturalsurvival.org/consent or cs.org/consent]
2. ufulu wa anthu a m’dera
Oyakhula oyamba:
Kuchokera pobadwa, munthu aliyense ali ndi ma ufulu ena omwe sangachotseledwe ndipo ngati
anthu a m’madera, tili ndi ufulu okhala, wachibadwidwe komanso wodziwitsidwa.
Oyankhula wachiwiri:
Sizimatengera kuti kaya ndiwe wadziko lanji, ufuluwu ndi wa tonse ndipo ukuyenera
kutsatilidwa pamene boma likufuna kuchita chilichonse ndi zithu za chilengedwe za m’dera
mwathu, makamaka ngati ncthitozo zikhonza kubweletsa kusintha komanso mavuto ku nthaka
yathu
3. kuwayimba milandu ma kampani
Oyankhula oyamba:
M’nyengo zonse ndimadandaula pa za kuchepa kwa zokolora zathu; tilibe minda yokwanira
kuyambira pomwe makampani adabwera ku dera kwathu.
Oyankhula wachiwiri:
Ndizoona, anatenga malo athu popanda chilolezo. Ufulu wachibadwidwe umatiteteze ife anthu
okhala m’madera ndipo limanenetsa kuti palibe ntchito yomwe ikuyenera kuchitika m’dera
mwathu popanda boma kapena ma kampani kutidziwitsa kaye, kutifunsa ndiponso kutimvera.
Tiyeni tichitepo kanthu kuwayimba mlandu makampani amenewa.
Okamba nkhani:
4. Atsogoleri
Oyankhula oyamba:
Ndine munthu wamba. Ndili ndi ufulu wochita zomwe ndafuna, ndi wodziwitsidwa zinthu
zisanachitike, koma boma limagwiritsa ntchito njira zambiri kuti liphwanye ufuluwu. Imodzi
mwanjirazi ndikupanga ziphuphu ndi mafumu, kuwapatsa ntchito, ndi malonjezo ena ndi ena
kuti achite zofuna za boma kapena makampani kusiya zofuna za anthu awo onse. Pa chifukwa
ichi, ndikwabwino kuti anthu adzisankha atsogoleri omwe amayikira kumtima mavuto a anthu
awo ndipo tidzigwira ntchito limodzi ndi atsogoleriwa potukula madera athu
5. Pangano la bungwe la UN, Gawo khumi
Oyankhula oyamba:
Kwa madera a anthu wamba, ufulu wachibadwidwe, kuchita chomwe wafuna komanso
kudziwitsidwa limalimbikitsidwa ndi gawo khumi la pangano la UN pa za ufulu wa anthu
wamba, lomwe limakamba kuti mayiko ndi maboma sangathamangitse anthu m’madera awo
kapena m’malo awo, ngakhale kuchita zomwe akufuna popanda chilolezo cha anthuwo.
6. Pangano la bungwe la UN, Gawo 19
Oyankhula oyamba:
(mawu a pansipansi) Gawo 19 la pangano la bungwe la UN pa za ufulu wa anthu a m’madera
limanena kuti (mawu omveka bwino bwino) boma likuyenera kulandira chilolezo kuchokera kwa
anthu lisanapange zilizonse zomwe zikhonza kuwasokoneza athuwo.
7. Madera a chitetezo
Oyankhula oyamba:
Monga anthu wamba, tili ndi ufulu okhala m’madera otetezedwa ndipo ngati kusitha
kungachitike m’madera mwathu, tiyang’ane gawo 29 la pangano la UN pa za ufulu wa anthu.
Panganoli limanena kuti: anthu am’madera akuyenera kupemphedwa komanso kuwuzidwa
zinthu zoopsa zisana sungidwe kapena kuponyedwa m’dera mwawo.
8. Ntchito za chitukuko.
Oyankhula oyamba:
(kuyankhulira pa chimkuza mawu) palibe kusintha komwe kungabweletsedwe
m’malo athu popanda kugwiritsa ncthito gawo 23 la pangano la UN pa za ufulu wa anthu lomwe
limanenetsa kuti boma likuyenera kupeza chilolezo kuchokera kwa anthu lisanavomereze ntchito
ina iliyonse ya chitukuko yomwe itha kuwasokonezera anthu nthaka yawo monga ntchito za
migodi, madzi ndi zinthu zina zotero.
9. Chithandizo Chochokera kunja
Oyankhula:
Monga anthu, tili ndi ufulu wosankha kusintha komwe kuti kuchitike m’dera mwathu. Monga
m’mene zinalembedwela mu pangano la bungwe la United Nations komanso gawo 169 la
bungwe lowona za anthu ogwira ntchito padziko lonse ndi ndondomeko zina zomwe
zimalemekeza ufulu wosakha zofuna komanso kudziwitsidwa. Ndondomekozi, zimalimbikitsa
ufulu wa anthuwu ndi kupempha mayiko kuti adzilemekeza ufulu wa anthu.
10. Ufulu wosatsutsika
Oyankhula oyamba:
Kwa anthu tonse, ufulu wochita zomwe tafuna, kudziwitsidwa zinthu zisanachitike ndi
wofunikira kwambiri, wachibadwidwe komanso osatsutsika. Izi zikuthandauza kuti, ndi ufulu
wofunika kwambiri ndi woyenera pa chitukuko ndipo sitingakane. Kutengera pa lamulo la dziko
lpnse lapansi, ufulu wochita zofuna ndi kudziwitsidwa zinthu zisana chitike ufuluwu
umawonetsetsa kuti anthu akuchita chisankho cha zitukuko zomwe akufuna mwaufulu kotero
kuti zipindulire iwo komanso mibadwo yomwe ikubwera kutsogolo molingana ndi chikhalidwe
chathu m’mene dziko lonse limaonera.
11. Kuphwanya ufulu wa anthu.
Control: Tinyimbo tomveka pansi pansi
Oyankhula oyamba:
Mwadzuka bwanji?
Oyankhula wachiwiri:
zikuyenda?
Oyankhula oyamba:
Chabwino zikomo. Mwamva zoti muli kampani yatsopano ntawuni? Ayamba
kulemba ntchito kwa anthu kuti ayambe zomanga manga m’mudzi mwathu muno.
Oyankhula wachiwiri:
chani? Sindimadziwa kalikonse…sindikukhulupilira zoti boma likupitilizabe
kupondereza ufulu wochita chomwe tafuna ndikudziwitsidwa womwe anthu ife tili nawo.
Akuyenera kutidziwitsa ndikumva maganizo athu ngati tikufuna chitukuko chimenechi
kapena ayi. Makamaka popeza kuti lamuloli ndilolembedwa momveka bwino
m’malamulo a dziko lino komanso malamulo a mayiko onse.
Oyankhula oyamba:
Inu ndiye mwanenetsa. Ndizachidziwikire kuti boma silikuchitapo kanthu
polimbikitsa izi. Ngati sitichitapo kanthu kuti boma lidzilemekeza ufulu wathu, maufulu
ndi malamulo omwe analembedwa adzingokhala penapake nkumachita fumbi
osamagwira ntchito yake. Makampani adzapitiliza kuphwanya ufulu wathu
ndikutengerapo mwayi kwa anthu wamba.
Oyankhula wachitatu:
Sitingalole ndipo sitidzalola kuti izi zichitike. Aphwanya ufulu wathu mokwanira.
Tiyeni timenyelele ufulu wathu poteteza dziko lapansi!
12. Thandauzo la kuchita chomwe ufuna
Control: Tinyimbo tomvekera pansi pansi
Oyankhula oyamba:
Ufulu wochita zomwe ufuna komanso kudziwitsidwa ndi ufulu omwe umakhudza
anthu onse pa nkhani za chitukuko m’madera athu.
Control: kanyimbo kopumira pang’ono (masekondi atatu)
Oyankhula wachiwiri:
Kuchita zomwe ufuna komanso kudziwitsidwa? Zikuthandauza chani mukamati
kuchita zomwe ufuna?
Control: kanyimbo kopumira pang’ono (masekondi atatu)
Oyankhula oyamba:
Gawo lochita chomwe ufuna limathandauza kuti boma silikuloredwa
kulowelerapo pa chisankho cha atsogoleri komanso anthu a m’madera chokhudza zoti
ngati akufuna zomanga manga m’dera lawo kapena ayi. Paazokambiranazi, anthu a
m’dera sangawumilizidwe mu njira iliyonse kuti avomereze maganizo ena ake. Izi
zikuphatikizapo kuwaopseza m’njira iliyonse, ziwawa, kugwiritsa ntchito udyo
mphamvu, katangale, ndi zina zotere. Ndizongofunika kuonetsetsa kuti pa zokambirana
zokhudza chitukuko pasakhale kuphwanya ufulu komwe tatchulaku kotero kuti boma
lidzilemekeza kwa ndthu ufulu wochita chome ufufna komanso kudziwitsidwa chinthu
chisana chitike..
Oyankhula wachiwiri:
Tikuyenera kuwumiliza kuti ufulu wochita chomwe tafuna ukhaledi woti
tidzichita chomwe tafuna.
13. Thandauzo la “Kudziwitsidwa zisanachitike”
Control : << phokoso la anthu pa zionetsero>
Oyankhula oyamba:
Galamukani! yimilirani! Palibenso nthawi ina yabwino kuposa ino kuti
tiwumilize boma kuti likhanzikitse ufulu wochita zomwe tafuna womwe unapelekedwa
kwa ife!
Control: kanyimbo kopumira pang’ono (masekondi atatu)
Oyankhula wachiwiri:
Mukudziwa, izi ndiye zikumveka. Zikhala kupita patsogolo kwakukulu ngati
boma lathu litavomereza za ufuflu wochita zomwe ufuna ndi kudziwitsidwa kwa
mtunthu. Chomwe chakhala chikusowa kwambiri ndi maganizo wodziwitsidwa chinthu
chisanachitike. Kudziwitsana kutachitika ntchito ya chitukuko isanayambe kapena
isanvomerezedwe ndi boma ndi njira. Zikuthandauza kuti tidzikhala ndi nthawi
yokwanira kwa anthu onse a m’dera kuti awunikire pa maganizo omwe apelekedwa.
Zoonadi! Tikuyenera kukhala ndi uthenga wokwanira ndinso womveka bwino
zitukukozi zisanayambe, kotero kuti titha kuzukuta ndikupanga maganizo athu ngati
anthu. Chinanso nchiyani, akuyenera adzigwira nafe ntchito limodzi pa gawo lililonse la
ntchitozo, mwachitsanzo pa kawuniwuni, kutsegulira komanso kutseka kwa ntchito za
migodi.
14. Thandauzo la "kudziwitsidwa”
Control: tinyimbo tomveka pansi pansi
Oyankhula oyamba:
Inu ndi ine, monga anthu okhala m’madera tili ndi ufulu wodziwitsidwa.
Control: kanyimbo kopumira pang’ono (masekondi atatu).
Ufuluwu ndiwofunikira pa chitukuko cha dera lililonse. Ichi ndi chifukwa chake
ukuyenera kukhanzikitsidwa kwa thunthu. Tiyeni tione zomwe zimathandauza tikamati
kudziwitsidwa. ‘Kudziwitsidwa’. Kukuthandauza kuti tili ndi ufulu olandira uthenga
wokwanira wokhudza chitukuko chomwe chikuyembekezeka kuchitika mu dera mwathu.
Izi zikuphatikizanso uthenga wokhudza ubwino ndi kuyipa ka ntchitozo ku za
chilengedwe komanso kwa anthu ndinso madera athu. Kafukufuku amene amachitidwa
pofuna kupeza uthengawu amatchedwa kuti “Environmental and Social Impact
Assessments”, kapena “ESIA” yemwe amayenera kuchitidwa ndi magulu oyima
pawokha wopanda m’gwirizano uliwonse ndi makampani. Uthenga wonse operekedwa
ukuyenera kukhala wokwanira, womveka bwino mchiyankhulo chathu, mogwirizana ndi
miyambo ndi chikhalidwe chathu ndi maganizidwe athu. Ndi udindo wathu kowonetsetsa
kuti ndife odziwitsidwa mokwanira maganizo omwe atha kukhudza anthu athu ndi malo
anthu asnapangidwe.
15. Ndiliti lomwe ufuluwu umagwira ntchito?
Oyankhula oyamba:
Mam’mawa wabwino, mulibwanji?
Oyankhula wachiwiri:
Ndili bwino zikomo. Eeh!, uli bwanji nkumano dzulo? Munakambirana zotani?
Oyakhula woyamba:
Zinalibwino kwambiri. Tinakambirana za ufulu wachibadwdwe, wochita zomwe
munthu ukufuna komanso wodziwitsidwa zinthu zisana chitike.
Oyankhula wachiwiri:
Koma chimenecho ndi chani? Mungafotokozeko zambiri?
Oyankhula oyamba:
Zimathandauza ufulu womwe anthu ife tili nawo kuti titetezere malo komanso
madera athu, ufulu womwe ndiwolembedwa m’malamulo woyendetsera dziko lino ndi
mayiko onse..
Oyankhula wachiwiri:
Ooh! chabwino, koma nanga tingawugwiritse ntchito bwanji ufuluwu? Ndipo
munyengo zotani?
Oyankhula woyamba:
Tikhonza ndipo tikuyenera kugwiritsa ntchito pa nthawi imene m’madera mwathu
mukuyembekezeka kuchitika zitukuko zosiyana siyana makamaka ngati pali chiopsezo
choononga chilengedwe. Popeza ndi ife amene timakhala m’maderawa komanso kuti
zotsatira zake zidzakhuza ife tomwe, zili ndi ife kuvomereza kuti zitukukozi zichitike
kapena ayi. Ufulu wachibadwidwe, wochita zomwe tafuna ndikudziwitsidwa kaye zinthu
zisanachitike umanenetsa kuti makampani akuyenera kutidziwitsa ndi kulemekeza
maganizo athu asanayambe kuchita chilichonse. Tikuyenera tiphunzire zambiri za izi.
Zikuwoneka ngati ndi zabwino kwambiri ku madera athu!
16. Udindo
Control: phokoso la kuchuna chuna kwa wayilesi (masekondi atatu)
Woyankhula woyamba:
Ufulu wachibadwidwe, wochita zofuna zathu komanso kudziwitsidwa chinthu
chisanachitike ndi ufulu womwe ife tilinawo monga anthu wamba pamene tikumenya
nkhondo yoteteza malo athu. Tikuyenera kukakamiza kuti ufulu wathu ulemekezedwe..
Control: kanyimbo kopumira pang’ono (masekondi atatu).
Oyankhula wachiwiri:
Agogo, tamverani zomwe akukamba pa wayilesi; kodi mukuganiza kuti ndi
chanzeru kwa anthu athu kuti amenyere nkhondo ufulu wathu wodziwitsidwa chinthu
chisana chitike?
Oyankhula wachitatu:
Ndi zoona, mwana wanga! Ufuluwu umateteza zinthu zathu zomwe; ufuluwu ubweletsa zabwino zambiri kwa anthu athu komanso dziko lonse lapansi. Dikira ndifotokoze: pogwiritsa ntchito ufulu umenewu, tikhonza kuteteza chilengedwe chathu ndikukhala ndi madzi a ukhondo ndo m’pweya wabwino zomwe zitha kuthandiza kuti mwina anthu athu adzikhala m’madera a ukhondo. Titha kuonetsetsa kuti ntchito za chitukukozi zitichitire ubwino osati kutiwononga.
Oyankhula wachiwiri:
Tsopano ndamvetsa Agogo! Izi ndi ndizothandiza kwabasi. Zikomo ko m’badwo wanu,
ndili ndi malo okhala aukhondo. Ndidzakwaniritsa udindo wanga wosamalira
chilengedwe kuti ndidzawasiyile ana anga komanso dzidzukulu malo abwino okhala.
17. Kugawanitsa ndi Kugonjetsa
Oyankhula woyamba:
Kugawanitsa ndi kugonjetsa. Ichi chakhala chida chomwe amakampani komanso
boma lakhala likugwiritsa ntchito pofuna kuchita zinthu m’madera. Ndi chimodzi mwa
dzitsanzo zomwe akhala akulephelera kulemekeza ufulu wa anthu wachibabwidwe
kuchita zofuna zawo komanso kudziwitsidwa chinthu chisana chitike. Malamulo a
padziko lonse akunenetsa kuti ma boma sakuyenera kutikakamiza kusintha maganizo,
miyambo ndi zikhalidwe zathu komanso njira zopangira ziganizo. Nthawi zambiri
makampani akulu akuluamayesetsa kupeza njira zophwanyila ufuluwu popeza amadziwa
kuti sitingavomereza zinthu zowononga chilengedwe ndi zomwe zitha kutisiya
m’mavuto. M’malo mwake amachita chinyengo ndi atsogoleri osiyana siyana m’madera
monga aphunzitsi, atsogoleri a mipingo, atsogoleri a ndale pogwiritsa ntchito uthenga
wabodza. Zittingasekelere zotere. Zili kwa ife kuonetsetsa kuti ufulu wathu
ukulemekezedwa kwathunthu. Sitidzalora kuti mtendere, umodzi komanso mphamvu za
mudzi wathu kuti zikhale pa chiopsezo chifukwa cha kugawikana ndi katangale.I
18. Mikumano ya m’madera
Oyankhula oyamba:
(mwachisoni) eeyi, zinthu zilibwanji?…
Oyankhula wachiwiri:
Zilibwino zikomo! Koma mukuwoneka wokhumudwa, chikuchitika ndi chiyani?
Oyankhula oyamba:
Ndakhumudwa kwambiri, ndakhala ndikumva mphekesera zokhudzana ndi
ntchito za migodi zomwe zakuyembekezeka kuchitika m’mudzi mwathu muno. Sibwino
popeza kuti anthu omwe akutsogolera sanatiuze ndikomwe zomwe zikuchitika.
Sakutsatira ufulu womwe tilinawo wochita zomwe tikufuna, komanso kudziwitsidwa
zinthu zisana chitike. Ndamvetsedwanso kuti boma likuyenera kukwaniritsa kwathunthu
ma ufulu amenewa ntchito za chitukuko ngati izi zikamachitika.x
Oyankhula wachiwiri:
Inu mukunena zoona. Tiyenera kuwonetsetsa kuti ufulu wathu ukulemekezedwa
potidziwitsa kaye ndikumva mbali yathu ntchito ngati izi zisanayambe. Mwachitsanzo pamene
ntchito ngati zomwezi zinabwera ku dera lakwathu, tinakumana ndikukambirana kuti tionetsetse
chilichonse chikamachitika ndipo tikuyenera kukhala ndi mphamvu zokwenyera makampani pa
zinthu zomwe adalonjeza ndi kuonetsetsa kuti akuchitadi ntchito zomwe tinagwirizana pa
zokambirana zathu. Ikanakhala ndondomeko yabwino kugwiritsa nchito m’dera lanu-
sitingapitilire kulolera kuti ntchitozi zipitilire ife tisakudziwapo kanthu
19. Zomwe ufulu wochita zofuna zathu, komanso kudziwitsidwa zinthu zisanachitike
umathandauza.
Oyankhula oyamba:
Kodi mukudziwa kuti ufulu wochita zofuna zanu, komanso kudziwitsidwa chinthu chisana
chitike umati chani?
Oyankhula wachiwiri:
Eya! Ndi ufulu womwe anthu wamba tilinawo wosankha chomwe tifuna kuti
chichitike pa malo athu.
Oyankhula oyamba:
Ndipo mukudziwa kuti titha kugwiritsa ntchito ufuluwu bwino lomwe m’madera
mwathu?
Oyankhula wachiwiri:
Hmm chabwino, koma sikweni kweni,
Oyankhula oyamba:
Monga anthu wamba okhala m’madera, ndi udindo wathu kufufuza uthenga
wokwanira wa ufulu umenewu, kotero kuti tisaponderezedwe ndi boma kapena
makampani. Kuti tipange ufuluwu kukhala woona, tikuyenera kumvetsetsa kuti ufuluwu
ndi wa anthu onse zomwe zikusonyeza kuti boma liyenera kulemekeza njira zomwe
timagwiritsa ntchito podziwitsana ndi kupanga zisankho za zomwe tikufuna.
Zikusonyezanso kuti oyimilira boma, makampani komanso midzi yathu akuyenera
kukumana pamodzi ndi kukambirana zokhudza chitukuko ndipo ife ndi amene tili ndi
mawu omaliza ndi cholinga chovomereza zitukuko zomwe zingapindulire madera athu.
20. Malangizo
Control: Nyimbo zamakolo pansi pansi
Oyankhula woyamba:
Kodi mukudziwa ndondomeko yomwe mukuyenera kutsatira kuti muonetsetse
kuti pali ufulu wochita chomwe mwafuna , komanso kudziwitsidwa chinthu
chisanachitike?
Control: kanyimbo kopumira pang’ono (masekondi atatu).
Oyankhula wachiwiri:
Kuti mudziwe kuti ufuluwu ndi wabwino kwa anthu tonse, tikuyenera kutsatira
ndondomeko izi pamene tikukumana ndi ntchito za chitukuko pa malo athu. Anthu
okhala m’maderawa akuyenera kudziwitsidwa kuyambira pa chiyambi. Nthawi
yokwanira ikuyenera kuperekedwa kuti dera lonse lilandire uthenga uliwonse wofunikira
wokhudza ubwino ndi kuipa kwa ntchito za chitukukozo ndi kupereka mpata kuti pakhale
zokambirana zikhudza mfundo zimenezi. Uthenga ukuyenera kuperekedwa pogwiritsa
ntchito njira zofalitsira uthenga zamakolo. Chiganizo chidzipangidwa popanda
kupondereza komanso kuopseza kwa oyang’anira chitukukocho. Zonse zomwe
mwagwirizana zikuyenera kulembedwa nd ikusungidwa bwino. Ngati ufulu
utaphwanyidwa kumbukuirani kuti pali njira zomwe tithakugwiritsa tchito pofuna kupeza
thandizo pa za kuphwanyidwa kwa ufuluwu pa dziko lonse lapansi kuchokera ku
mabungwe monga la United Nations.
Kuti mudziwe zambiri pitani pa. cultural survival dot org slash consent
[culturalsurvival.org/consent or cs.org/consent]