2
Develop Malawi, Pay Taxes Malawi Revenue Authority Msonkho House Independence Drive Private Bag 247 Blantyre Tel: +265 - 1 822 588 Fax: +265 - 1 822 302 E-mail: [email protected] Web: www.mra.mw Produced by Corporate Affairs Division - MRA Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mukukayikira kuti anthu ena akuzembetsa katundu? Ngati mukukayikira kuti anthu ena akuzembetsa katundu, muyenera kukanena ku office ya MRA kapena Police yomwe muli nayo pafupi. Ngati munthu ozembetsa katundu wakupemphani kuti mumuthandize kunyamula kapena kusunga katundu, kanani ndipo muyenera kukamuneneza ku office ya MRA kapena ku Police yomwe muli nayo pafupi. Ngati mungathandize munthu yemwe akuzembetsa katundu, pompatsa malo ogona kapena kumunyamulira katundu wake ndiye kuti mukuthandiza polibera Boma ndalama zomwe zinakatha kugwira ntchito zina za chitukuko. Dziwani kuti kuthandiza munthu kuzembetsa katundu ndiye kuti mukumupangitsa munthuyo kuti akhale olemera pomwe inu mukusowa chitukuko kudera lanu ndikumasauka ZOYENERA KUCHITA POFUNA KUWOMBOLA KATUNDU PA BODA NDI KUIPA KWA SIMAGO July 2016 - June 2017 Kumvesetsa Za...

Kumvesetsa Za - Malawi Revenue Authority - Home...• Munthu amauzidwa kuti alipire chindapusa chosachepera MK100,000 kapena katatu kuposera apo • Munthu atha kutengeredwa ku khoti

  • Upload
    others

  • View
    2

  • Download
    0

Embed Size (px)

Citation preview

  • Develop Malawi, Pay Taxes

    Malawi Revenue AuthorityMsonkho HouseIndependence DrivePrivate Bag 247Blantyre

    Tel: +265 - 1 822 588Fax: +265 - 1 822 302E-mail: [email protected]: www.mra.mw

    Produced by Corporate Affairs Division - MRA

    Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mukukayikira kuti anthu ena akuzembetsa katundu?Ngati mukukayikira kuti anthu ena akuzembetsa katundu, muyenera kukanena ku office ya MRA kapena Police yomwe muli nayo pafupi. Ngati munthu ozembetsa katundu wakupemphani kuti mumuthandize kunyamula kapena kusunga katundu, kanani ndipo muyenera kukamuneneza ku office ya MRA kapena ku Police yomwe muli nayo pafupi.

    Ngati mungathandize munthu yemwe akuzembetsa katundu, pompatsa malo ogona kapena kumunyamulira katundu wake ndiye kuti mukuthandiza polibera Boma ndalama zomwe zinakatha kugwira ntchito zina za chitukuko.

    Dziwani kuti kuthandiza munthu kuzembetsa katundu ndiye kuti mukumupangitsa

    munthuyo kuti akhale olemera pomwe inu

    mukusowa chitukuko kudera lanu ndikumasauka

    ZOYENERA KUCHITA POFUNA KUWOMBOLA KATUNDU PA BODA NDI

    KUIPA KWA SIMAGO

    July 2016 - June 2017

    Kumvesetsa Za...

  • Kodi anthu akafika pa boda ndi katundu kuchokera kunja ayenera kutani?

    Munthu akafika pa boda ayenera kutsata ndondomeko izi:

    • Adzapatsidwa fomu 47 yomwe akuyenera kulembapo katundu yense yemwe wafika naye

    • Ma ofisala a MRA akhonza kuyang’ana katundu wanu kuti atsimikize ngati zomwe mwalemba pa fomu zikufanana ndi katundu yemwe mwabweretsa

    • Katundu yemwe mtengo wake ukupitirila K500,000 ayenera kuomboledwa podzera kwa ma clearing agents (othandiza kuwombola katundu) omwe amagwiritsa ntchito Fomu 12

    • Ndi mlandu kupereka mapepara a bodza owonetsa mtengo omwe mwagulira katundu

    Kodi munthu angadziwe bwanji za msonkho omwe akuyenera kulipira pa katundu yemwe wagula kunja?

    Bungwe la MRA limagwiritsa ntchito bukhu lotchedwa Tariff lomwe limalongosola za msonkho omwe mukuyenera kupereka malingana ndi katundu amene mwabweretsa. Musanayitanitse katundu ndibwino kufunsa ku ofesi ya Customs kuti akufotokozereni za misonkho yomwe mukuyenera kulipira pa katundu amene mukuyembekezera kubweretsa.

    Katundu osiyanasiyana amakhalanso ndi milingo yosiyanasiyana yowerengetsera msonkho. Mwachitsanzo, katundu monga fodya, mowa ndi galimoto ziri ndi milingo yosiyanasiyana ya msonkho yomwe imakhala yokwelerapo

    Pamene munthu wagula katundu ku mayiko omwe ali pamgwirizano wa malonda ndi dziko lino, malingana ndi mgwirizanowu, munthu amakhala ndi mwawi kulipira msonkho ochepa. Izi zimatheka pamene mwaonetsa zikalata zaumboni zosonyeza kuti katunduyo wapangidwadi m’dziko limenelo.

    Kodi Simago ndi chiyani?Simago ndi mchitidwe wozembetsa katundu kuchokera kunja kubweretsa mdziko muno kapena kutulutsa katundu kunja mwachinyengo komanso

    posadzera pa boda. Kuzembetsa katundu kumachitika mnjira zosiyanasiyana monga izi:

    • Kuonetsa katundu ochepa pa boda wina nkubisa• Kupereka malisiti kapena ma invoisi onama kapena a

    feki ndi cholinga chofuna kulipira msonkho wochepa kapena kusalipira kumene

    • Kudutsitsa katundu njira zosavomerezeka ndi Boma

    Kodi kuipa kwa Simago kapena kuzembetsa katundu ndi kotani?

    Kuipa kwa Simago ndi uku:

    • Boma silitolera msonkho woyenera pa chifukwa ichi chitukuko cha dziko chimalowa pansi

    • Simago imapangitsa kuti katundu osaloledwa monga mfuti, mabomba, mankhwala wosokoneza bongo kapena katundu wotha mphamvu (expire) alowe mdziko muno ndikuika miyoyo ya anthu pa chiwopyezo

    • Makampani ena atha kutsekedwa chifukwa katundu wopangidwa simagoyo amagulitsidwa pa mtengo wotsika kamba koti sanalipire msonkho pa boda

    • Boma silimatha kupanga kalondolondo woyenera pa katundu amene akulowa ndipo izi zimapangitsa kuti Boma lipange ndondomeko zosayenera

    Nanga chilango cha kuzembetsa katundu ndi chotani?• A MRA amalanda katunduyo ndikumusunga mpaka

    ataomboledwa• Munthu amauzidwa kuti alipire chindapusa

    chosachepera MK100,000 kapena katatu kuposera apo

    • Munthu atha kutengeredwa ku khoti ndipo akapezeka wolakwa amatsekeledwa kundende ndi kukagwira ukaidi wakalavula gaga kopitilira zaka zitatu