16
MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE YAMBANI KUPHUNZIRA BAIBULO

MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

  • Upload
    others

  • View
    184

  • Download
    18

Embed Size (px)

Citation preview

Page 1: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

MUNGAKHALE ND I MOYOMPAKA KALEKALE

YA M B A N I K U P H U N Z I R A B A I B U L O

Page 2: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

Tonsefe timadzifunsa mafunso okhudza moyo,kuvutika, imfa komanso tsogolo lathu. Tima-funanso titadziwa zimene tingachite kuti titha-ne ndi mavuto amene timakumana nawo tsikundi tsiku, monga kusapeza ndalama zokwanirandiponso zimene tingachite kuti tizikhala mo-sangalala m’banja lathu. Anthu ambiri amaonakuti Baibulo limawathandiza kupeza mayankhoa mafunso ofunika komanso amapezamo mala-ngizo odalirika. Kunena zoona, Baibulo likhozakuthandiza munthu wina aliyense.

1. Kodi ndi mafunso ena ati amene Baibulolimayankha?Baibulo limayankha mafunso ofunika mongaakuti: Kodi moyo unayamba bwanji? Kodi cho-linga cha moyo n’chiyani? N’chifukwa chiya-ni anthu abwino amavutika? Kodi chimachitikan’chiyani munthu akamwalira? Popeza aliyenseamafuna mtendere, n’chifukwa chiyani padzikoli

pamachitika nkhondo? N’chiyani chidzachi-tikire dzikoli kutsogoloku? Baibulo limatilimbi-kitsa kuti tizipeza mayankho a mafunso ngatiamenewa ndipo anthu mamiliyoni ambiri apezamayankho ogwira mtima a mafunsowa.

2. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji kutitizisangalala?M’Baibulo muli malangizo abwino. Mwachitsa-nzo, limafotokoza zimene mabanja angachi-te kuti azikhaladi mosangalala. Limapereka-nso malangizo othandiza kuti tisamade nkhawakwambiri komanso kuti tizikonda ntchito yathu.Tikamakambirana zimene zili m’bukuli, muphu-nzira zimene Baibulo limanena pa nkhani ngatizimenezi ndi zinanso. Mudzafika pomvetsa kuti“Malemba onse [kapena kuti mawu onse ame-ne ali m’Baibulo] . . . ndi opindulitsa.”—2 Timo-teyo 3:16.

01

Kodi BaibuloLingakuthandizeni Bwanji?

Bukuli silikulowa m’malo mwa Baibulo. Koma likuthandizani kuti muzifufuza mfundo za m’Baibulopanokha. Choncho tikukulimbikitsani kuti muziwerenga malemba amene aikidwa m’phunziro lililo-nse, kenako muziwayerekezera ndi zimene mukuphunzira.

5

F U F U Z A N I M O Z A M A

Fufuzani mmene Baibulo lathandizira anthu ena, zimene mungachitekuti muzisangalala poliwerenga ndiponso ubwino wopempha anthu enakuti akuthandizeni kulimvetsa.

3. Baibulo lingatithandizeBaibulo lili ngati nyale yowala kwambiri. Lingatithandize kuti tizisankhazinthu mwanzeru, komanso limatiuza zimene zichitike m’tsogolo.Werengani Salimo 119:105, kenako mukambirane mafunso awa:

˙ Kodi amene analemba salimoli, ankaliona bwanji Baibulo?˙ Nanga inuyo mumaliona bwanji?

4. Baibulo limayankha mafunso athuBaibulo linathandiza mayi wina kupeza mayankho a mafunso ameneankamuvutitsa maganizo kwa zaka zambiri. Onerani VIDIYO, kena-ko mukambirane mafunso otsatirawa.

˙ Kodi muvidiyoyi, mayiyu anali ndi mafunso otani?˙ Nanga kuphunzira Baibulo kunamuthandiza bwanji?

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizifunsa mafunso.WerenganiMateyu 7:7, ndipo kenako kambiranani funso ili:

˙ Kodi muli ndi mafunso otani amene mukufuna kuti Baibulolikuyankheni?

VIDIYO: Musataye Mtima!(1:48)

(

5. Mukhoza kumasangalalapowerenga BaibuloAnthu ambiri amasangalala powerenga Baibulo ndipo likuwatha-ndiza kwambiri. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunsootsatirawa.

˙ Muvidiyoyi, kodi achinyamatawa ankaiona bwanji nkhaniyowerenga mabuku?

˙ Ngakhale kuti sakonda kuwerenga mabuku, n’chifukwachiyani amakonda kuwerenga Baibulo?

Baibulo limatipatsa malangizo amene amatitonthoza komansokutipatsa chiyembekezo. Werengani Aroma 15:4, kenakomukambirane funso ili:

˙ Kodi mungakonde kumva uthenga wa m’Baibulo womweumatitonthoza komanso kutipatsa chiyembekezo?

6. Anthu ena akhoza kutithandizakulimvetsa bwino BaibuloKuwonjezera pa kuwerenga Baibulo paokha, anthu ambiri amaonakuti kukambirana ndi ena kumawathandiza kuti azilimvetsa bwino.Werengani Machitidwe 8:26-31, kenako mukambirane funso ili:

˙ Kodi tingatani kuti tizilimvetsa bwino Baibulo?—Onanimavesi 30 ndi 31.

VIDIYO: Kuwerenga Baibulo(2:05)

ZIMENE ENA AMANENA: “Kuphunzira Baibulo ndi kutaya nthawi.”

˙ Inuyo mukuganiza bwanji? Nanga n’chifukwa chiyani mukutero?

(

Munthu wina wa ku Itiyopiyaankafunika kuthandizidwa ndimunthu wina kuti amvetse Malemba.Masiku ano anthu ambiri amaonakuti ndi bwino kuti anthu enaawathandize kulimvetsa bwinoBaibulo

7

ZOMWE TAPHUNZIRABaibulo limatipatsa malangizo otha-ndiza, limayankha mafunso ofunikakwambiri, komanso limatitonthozandi kutipatsa chiyembekezo.

Kubwereza˙ Kodi m’Baibulo mumapezekamalangizo otani?

˙ Kodi ndi mafunso ena atiamene Baibulo limayankha?

˙ Kodi ndi zinthu ziti zomwemungakonde kuphunziram’Baibulo?

Tsiku limene tamaliza phunziroli

ZolingaN Kuwerenga mbali yoyamba

ya phunziro lotsatira.

N Zina:

O N A N I Z I N A N S O

Onani mmene malangizoa m’Baibulo akuthandiziraanthu masiku ano.“Mfundo za M’BaibuloSizikalamba”(Nsanja ya OlondaNa. 1 2018)

Onani mmene Baibulo linatha-ndizira munthu wina ameneanali ndi vuto lodzikayikirakuyambira ali wamng’onoMmene Ndinayambira Kukhalandi MoyoWosangalala

( 2:53

Onani malangizo a m’Baibuloothandiza kuti banja liziyendabwino.“Mfundo 12 ZothandizaKuti Banja Liziyenda Bwino”(Galamukani! Na. 2 2018)

Onani zimene Baibulo limanenapa nkhani ya amene akulamuli-ra dzikoli ngakhale kuti anthuambiri ali ndi maganizo olakwi-ka pa nkhaniyi.N’chifukwa Chiyani TiyeneraKuphunzira Baibulo?—VidiyoYathunthu

( 3:14

Kuti mupeze mavidiyo ndi zinthu zina zogwiritsa ntchito muPHUNZIRO 01, pangani sikani kachidindo aka kapena tsegulanibuku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale pa jw.org

Zimene mungachite kuti muzipindulandi phunziro lililonse

Pezani munthu woti azikuphunzitsani: Pemphani wa Mboni za Yehova kuti azikuphunzitsaniBaibulo kapena lembani fomu pawebusaiti yathu ya jw.org.

MBALI YOYAMBAWerengani ndime iliyonsekuphatikizapo mafunso (A)komanso malemba (B) omweakutsindika mfundo zikuluzi-kulu. Malemba amenealembedwa kuti “werengani”muziwawerenga mokwezamukamaphunzira ndimphunzitsi wanu.

MBALI YAPAKATIMawu oyamba (C) omwe ali pansi pa kamutukakuti Fufuzani Mozama akufotokoza mfundozomwe mutakambirane. Mitu ing’onoing’ono(D) ikufotokozera mfundo zazikulu zomwe zilim’phunziro lililonse. Werengani malemba, yankhanimafunso ndi kuonera mavidiyo (E). Onetsetsanizithunzi ndi mawu ake (F) ndipo ganizirani mmenemungayankhire Zimene Ena Amanena (G).

MBALI YOMALIZAMalizani phunziro lililonsepokambirana mbali ya ZomweTaphunzira komanso Kubwe-reza (H). Lembani tsikulimene mwamaliza phunziro.Mbali yakuti Zolinga (I), ilindi zoti muchite kuti mupiti-rizebe kuphunzira kapenansomugwiritse ntchito zomwemwaphunzira. Pansi pa mutuwakuti Onani Zinanso palizinthu zina zomwe mungako-nde kuwerenga kapenansokuonera.

Mmene mungapezere malemba m’Baibulo

Malemba asonyezedwa ndi buku la m’Baibulo (A), chaputala (B)ndi vesi kapena mavesi (C). Mwachitsanzo, Yohane 17:3 akutanthauzabuku la Yohane, chaputala 17 vesi 3.

A

B

C

D

E

F

G

H

I

J

mukumana ndi masautso, koma limbanimtima. Ine ndaligonjetsa dziko.”

17 Yesu atalankhula zinthu zimene-zi, anakweza maso ake kumwa-

mba ndi kunena kuti: “Atate, nthawiyafika, lemekezani mwana wanu, kutimwana wanu akulemekezeni. 2 Inumwamupatsa ulamuliro pa anthu onse,kuti onse amene inu mwamupatsa, awa-patse moyo wosatha. 3 Pakuti moyowosatha adzaupeza akamaphunzira ndikudziwa za inu, Mulungu yekhayo ame-ne ali woona, ndi za Yesu Khristu, ame-ne inu munamutuma. 4 Ndakulemeke-zani padziko lapansi, popeza ndatsirizakugwira ntchito imene munandipatsa.5 Ndipo tsopano Atate, ndiloleni kuti

YOHANE 16:33—17:24�A

�B

�C

Page 3: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

Tonsefe timadzifunsa mafunso okhudza moyo,kuvutika, imfa komanso tsogolo lathu. Tima-funanso titadziwa zimene tingachite kuti titha-ne ndi mavuto amene timakumana nawo tsikundi tsiku, monga kusapeza ndalama zokwanirandiponso zimene tingachite kuti tizikhala mo-sangalala m’banja lathu. Anthu ambiri amaonakuti Baibulo limawathandiza kupeza mayankhoa mafunso ofunika komanso amapezamo mala-ngizo odalirika. Kunena zoona, Baibulo likhozakuthandiza munthu wina aliyense.

1. Kodi ndi mafunso ena ati amene Baibulolimayankha?Baibulo limayankha mafunso ofunika mongaakuti: Kodi moyo unayamba bwanji? Kodi cho-linga cha moyo n’chiyani? N’chifukwa chiya-ni anthu abwino amavutika? Kodi chimachitikan’chiyani munthu akamwalira? Popeza aliyenseamafuna mtendere, n’chifukwa chiyani padzikoli

pamachitika nkhondo? N’chiyani chidzachi-tikire dzikoli kutsogoloku? Baibulo limatilimbi-kitsa kuti tizipeza mayankho a mafunso ngatiamenewa ndipo anthu mamiliyoni ambiri apezamayankho ogwira mtima a mafunsowa.

2. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji kutitizisangalala?M’Baibulo muli malangizo abwino. Mwachitsa-nzo, limafotokoza zimene mabanja angachi-te kuti azikhaladi mosangalala. Limapereka-nso malangizo othandiza kuti tisamade nkhawakwambiri komanso kuti tizikonda ntchito yathu.Tikamakambirana zimene zili m’bukuli, muphu-nzira zimene Baibulo limanena pa nkhani ngatizimenezi ndi zinanso. Mudzafika pomvetsa kuti“Malemba onse [kapena kuti mawu onse ame-ne ali m’Baibulo] . . . ndi opindulitsa.”—2 Timo-teyo 3:16.

01

Kodi BaibuloLingakuthandizeni Bwanji?

Bukuli silikulowa m’malo mwa Baibulo. Koma likuthandizani kuti muzifufuza mfundo za m’Baibulopanokha. Choncho tikukulimbikitsani kuti muziwerenga malemba amene aikidwa m’phunziro lililo-nse, kenako muziwayerekezera ndi zimene mukuphunzira.

3

Page 4: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

F U F U Z A N I M O Z A M A

Fufuzani mmene Baibulo lathandizira anthu ena, zimene mungachitekuti muzisangalala poliwerenga ndiponso ubwino wopempha anthu enakuti akuthandizeni kulimvetsa.

3. Baibulo lingatithandizeBaibulo lili ngati nyale yowala kwambiri. Lingatithandize kuti tizisankhazinthu mwanzeru, komanso limatiuza zimene zichitike m’tsogolo.Werengani Salimo 119:105, kenako mukambirane mafunso awa:

˙ Kodi amene analemba salimoli, ankaliona bwanji Baibulo?˙ Nanga inuyo mumaliona bwanji?

4. Baibulo limayankha mafunso athuBaibulo linathandiza mayi wina kupeza mayankho a mafunso ameneankamuvutitsa maganizo kwa zaka zambiri. Onerani VIDIYO, kena-ko mukambirane mafunso otsatirawa.

˙ Kodi muvidiyoyi, mayiyu anali ndi mafunso otani?˙ Nanga kuphunzira Baibulo kunamuthandiza bwanji?

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizifunsa mafunso.WerenganiMateyu 7:7, ndipo kenako kambiranani funso ili:

˙ Kodi muli ndi mafunso otani amene mukufuna kuti Baibulolikuyankheni?

VIDIYO: Musataye Mtima!(1:48)

(

Page 5: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

5. Mukhoza kumasangalalapowerenga BaibuloAnthu ambiri amasangalala powerenga Baibulo ndipo likuwatha-ndiza kwambiri. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunsootsatirawa.

˙ Muvidiyoyi, kodi achinyamatawa ankaiona bwanji nkhaniyowerenga mabuku?

˙ Ngakhale kuti sakonda kuwerenga mabuku, n’chifukwachiyani amakonda kuwerenga Baibulo?

Baibulo limatipatsa malangizo amene amatitonthoza komansokutipatsa chiyembekezo. Werengani Aroma 15:4, kenakomukambirane funso ili:

˙ Kodi mungakonde kumva uthenga wa m’Baibulo womweumatitonthoza komanso kutipatsa chiyembekezo?

6. Anthu ena akhoza kutithandizakulimvetsa bwino BaibuloKuwonjezera pa kuwerenga Baibulo paokha, anthu ambiri amaonakuti kukambirana ndi ena kumawathandiza kuti azilimvetsa bwino.Werengani Machitidwe 8:26-31, kenako mukambirane funso ili:

˙ Kodi tingatani kuti tizilimvetsa bwino Baibulo?—Onanimavesi 30 ndi 31.

VIDIYO: Kuwerenga Baibulo(2:05)

ZIMENE ENA AMANENA: “Kuphunzira Baibulo ndi kutaya nthawi.”

˙ Inuyo mukuganiza bwanji? Nanga n’chifukwa chiyani mukutero?

(

Munthu wina wa ku Itiyopiyaankafunika kuthandizidwa ndimunthu wina kuti amvetse Malemba.Masiku ano anthu ambiri amaonakuti ndi bwino kuti anthu enaawathandize kulimvetsa bwinoBaibulo

5

Page 6: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

ZOMWE TAPHUNZIRABaibulo limatipatsa malangizo otha-ndiza, limayankha mafunso ofunikakwambiri, komanso limatitonthozandi kutipatsa chiyembekezo.

Kubwereza˙ Kodi m’Baibulo mumapezekamalangizo otani?

˙ Kodi ndi mafunso ena atiamene Baibulo limayankha?

˙ Kodi ndi zinthu ziti zomwemungakonde kuphunziram’Baibulo?

Tsiku limene tamaliza phunziroli

ZolingaN Kuwerenga mbali yoyamba

ya phunziro lotsatira.

N Zina:

O N A N I Z I N A N S O

Onani mmene malangizoa m’Baibulo akuthandiziraanthu masiku ano.“Mfundo za M’BaibuloSizikalamba” (Nsanja ya OlondaNa. 1 2018)

Onani mmene Baibulo linatha-ndizira munthu wina ameneanali ndi vuto lodzikayikirakuyambira ali wamng’onoMmene Ndinayambira KukhalaNdi MoyoWosangalala

( 2:53

Onani malangizo a m’Baibuloothandiza kuti banja liziyendabwino.“Mfundo 12 ZothandizaKuti Banja Liziyenda Bwino”(Galamukani! Na. 2 2018)

Onani zimene Baibulo limanenapa nkhani ya amene akulamuli-ra dzikoli ngakhale kuti anthuambiri ali ndi maganizo olakwi-ka pa nkhaniyi.N’chifukwa Chiyani TiyeneraKuphunzira Baibulo?—VidiyoYathunthu

( 3:14

Kuti mupeze mavidiyo ndi zinthu zina zogwiritsa ntchito muPHUNZIRO 01, pangani sikani kachidindo aka kapena tsegulanibuku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale pa jw.org

Page 7: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

Anthu padziko lonse amakumana ndi mavu-to amene amawachititsa kukhumudwa, kudankhawa komanso kumva kupweteka. Kodi inu-nso munakumanapo ndi vuto limene linakuchi-titsani kumva chonchi? Mwina panopa muku-dwala kapena munthu amene mumamukondaanamwalira. Mwina mukudzifunsa kuti, ‘Komazinthu zidzakhalanso bwino?’ Baibulo limaya-nkha mogwira mtima funso limeneli.

1. Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kukhalandi chiyembekezo?Baibulo silimangofotokoza chifukwa chake pa-dzikoli pali mavuto ochuluka chonchi, koma li-matiuzanso uthenga wabwino wakuti posa-chedwapa mavuto onsewa adzatha. ZimeneBaibulo limalonjeza zingatithandize kukhala ndi“chiyembekezo chabwino ndiponso tsogololabwino.” (Werengani Yeremiya 29:11, 12.) Zi-menezi zimatithandiza kuti tizitha kupirira ma-vuto, tiziona zinthu moyenera ndiponso kuti ti-dzakhale osangalala mpaka kalekale.

2. Kodi Baibulo limafotokoza kuti m’tsogolomumudzachitika zotani?Baibulo limanena kuti m’tsogolomu “imfa si-dzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, ka-pena kubuula, ngakhale kupweteka.” (We-rengani Chivumbulutso 21:4.) Mavuto amene

tikukumana nawo masiku ano monga umpha-wi, kupanda chilungamo, matenda komansoimfa sadzakhalaponso. Baibulo limalonjeza kutianthu adzakhala ndi moyo wosatha m’Paradai-so padziko lapansi.

3. Kodi inuyo mungatani kuti muzikhulupirirakwambiri zimene Baibulo limalonjeza?Anthu ambiri amafuna zinthu zabwino zitachiti-ka, koma sakhulupirira ndi mtima wonse kuti zi-dzachitikadi. Koma zimene Baibulo limalonjezan’zosiyana ndi zimenezi. Tingakhulupirire kwa-mbiri zimene Baibulo limanena ngati tikuyese-tsa “kufufuza Malemba mosamala.” (Machiti-dwe 17:11) Mukamaphunzira Baibulo, mudziwazimene limanena zokhudza m’tsogolo. Ndiye zilindi inu kuzikhulupirira kapena ayi.

02

Baibulo LimatithandizaKukhala Ndi Chiyembekezo

7

Page 8: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

F U F U Z A N I M O Z A M A

Fufuzani zinthu zina zimene Baibulolimalonjeza zokhudza m’tsogolo ndipoonani mmene chiyembekezo chotchuli-dwa m’Baibulo chikuthandizira anthumasiku ano.

4. Baibulo limatilonjeza moyo wosathakomanso wangwiroTaonani malonjezo otsatirawa amene amapezeka m’Baibulo. Kodi ndi malonjezo atiamene akusangalatsani kwambiri? Nanga n’chifukwa chiyani mukutero?

Werengani malemba amene ali pa lonjezo lililonse, kenako yankhani mafunso awa:

˙ Kodi malemba amenewa akukupatsani chiyembekezo? Nanga angathandizensoanthu a m’banja lanu ndi anzanu kukhala ndi chiyembekezo?

Yerekezerani kuti muli m’dziko lomwe

PALIBE ALIYENSE AMENE . . .

˙ akumva kupweteka, kuvutika ndiukalamba kapena kumwalira.—Yesaya 25:8.

˙ akudwala kapena kulumala.—Yesaya 33:24; 35:5, 6.

˙ akuchitiridwa zinthuzopanda chilungamo.—Yesaya 32:16, 17.

˙ akuvutika ndi nkhondo.—Salimo 46:9.

˙ akuvutika maganizo kapena kuku-mbukira mavuto.—Yesaya 65:17.

ALIYENSE ADZAKHALA NDI MWAYI . . .

˙ woona anthu amene anamwaliraakuukitsidwa padziko lapansi.—Yohane 5:28, 29.

˙ wokhala ndi thanzi labwino komansomphamvu.—Yobu 33:25.

˙ wokhala ndi chakudya chokwanira, nyumbayabwino komanso ntchito yosangalatsa.—Salimo 72:16; Yesaya 65:21, 22.

˙ wokhala mwamtendere mpaka kalekale.—Salimo 37:11.

˙ wokhala ndi moyo wosatha m’dziko labwinokwambiri.—Salimo 37:29.

Page 9: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

5. Malonjezo a m’Baibuloangakuthandizeni panopaAnthu ambiri amakhumudwa kapenanso kukwiya akaonamavuto amene ali m’dzikoli. Anthu ena amayesetsa kumenye-ra ufulu kuti zinthu zisinthe. Onani mmene malonjezo a m’Bai-bulo akuti zinthu zidzasintha akuthandizira anthu masiku ano.Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

˙ Muvidiyoyi, kodi ndi zinthu ziti zopanda chilungamozimene zinkamupweteka kwambiri Rafika?

˙ Ngakhale kuti zinthu zopanda chilungamozo sizinathe,kodi Baibulo linamuthandiza bwanji?

Zimene Baibulo limatilonjeza zimatithandiza kukhala ndichiyembekezo chabwino ndipo timasiya kukhumudwa n’kuma-pirira mavuto athu bwinobwino. Werengani Miyambo 17:22ndi Aroma 12:12, kenako mukambirane mafunso awa:

˙ Kodi mukuganiza kuti uthenga wa chiyembekezo wope-zeka m’Baibulo ungakuthandizeni pamoyo wanu masikuano? N’chifukwa chiyani mukutero?

VIDIYO: Ndinkafunitsitsa KuthanaNdi Kupanda Chilungamo (4:07)

ZIMENE ENA AMANENA: “Zimene Baibulo limalonjeza ndi zabwino kwambiri, koma sizingatheke.”

˙ N’chifukwa chiyani muyenera kufufuza umboni wakuti zimene Baibulo limalonjeza zidzachitikadi?

(

9

Page 10: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

ZOMWE TAPHUNZIRABaibulo limatithandiza kukhala ndichiyembekezo ndipo limatilonjeza kutitidzasangalala m’tsogolo. Zimenezizimatithandiza kuti tipirire mavutoathu panopa.

Kubwereza˙ N’chifukwa chiyani anthu akufu-nika kukhala ndi chiyembekezo?

˙ Kodi Baibulo limati m’tsogolomudzachitika zotani?

˙ Kodi kukhala ndi chiyembekezokungatithandize bwanji masikuano?

Tsiku limene tamaliza phunziroli

ZolingaN Kuwerenga mavesi onse

amene ali m’phunziroli kutindidziwe bwino malonjezoa m’Baibulo.

N Zina:

O N A N I Z I N A N S O

Onani mmene chiyembekezochingakuthandizireni mukakha-la pa mavuto.“Kodi ChiyembekezoMungachipeze Kuti?”(Galamukani!, May 8, 2004)

Onani mmene kuyembekezerazinthu zabwino za m’tsogolokungathandizire anthu ameneakudwala.“Kodi Baibulo Lingandithandi-ze Kupirira Matenda?” (Nkhaniyapawebusaiti)

Mukamaonera nyimboyi,muziganizira mmene inuyo ndibanja lanu mudzasangalalirendi moyo m’Paradaiso ameneBaibulo linalonjeza.Ganizira Nthawiyo

( 3:37

Onani mmene munthu winayemwe ankamenyera ufulu waanthu ndi zinyama anasinthiramoyo wake atangophunzirazimene Baibulo limalonjezazokhudza m’tsogolo.“Panopa Ndilibenso MaganizoOfuna Kusintha ZinthuM’dzikoli” (Nsanja ya Olonda,July 1, 2013)

Kuti mupeze mavidiyo ndi zinthu zina zogwiritsa ntchito muPHUNZIRO 02, pangani sikani kachidindo aka kapena tsegulanibuku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale pa jw.org

Page 11: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

Baibulo limapereka malonjezo komanso mala-ngizo ambirimbiri. N’kutheka kuti mumafunakudziwa zimene limaphunzitsa, koma mwinansomumachita mantha. Kodi ndi bwino kukhulu-pirira zimene buku lakale chonchi limalonjezakomanso malangizo amene limapereka? Nangandi nzeru kukhulupirira zimene Baibulo limane-na zoti n’zotheka kukhala wosangalala panopakomanso m’tsogolo? Anthu ambiri amakhulupi-rira zimenezi. Tiyeni tione ngati inunso mungazi-khulupirire.

1. Kodi zimene Baibulo limanena ndi zoonakapena n’zongopeka?Baibulo limanena kuti uthenga wake ndi “mawuolondola a choonadi.” (Mlaliki 12:10) Limafo-tokoza nkhani zenizeni zokhudza anthu enie-ni. (Werengani Luka 1:3; 3:1, 2.) Anthu ofufuzambiri yakale komanso asayansi apeza umboniwakuti madeti, mayina a anthu, malo ndiponsonkhani za m’Baibulo ndi zolondola.

2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulosilinathe ntchito?Olemba Baibulo analemba mfundo zimene panthawiyo ambiri sankazidziwa. Mwachitsanzo,limatha kufotokoza molondola zinthu zokhudza

sayansi. Pa nthawi imene ankalemba zimenezianthu anali asanadziwe zoona zake pa nkhani-zo. Koma asayansi apanopa atsimikizira kuti zi-mene Baibulo limanena ndi zolondola. Mawu am’Baibulo “ndi odalirika . . . mpaka kalekale.”—Salimo 111:7, 8.

3. N’chifukwa chiyani tingakhulupirire zimeneBaibulo limanena zokhudza m’tsogolo?M’Baibulo muli maulosi� a “zinthu zimene sizi-nachitike.” (Yesaya 46:10) Linaneneratu nkhanizina kutatsala zaka zambirimbiri kuti zichitike.Linaneneratunso ndendende mmene moyo uli-li padzikoli masiku ano. M’mutuwu tikambira-na maulosi ena a m’Baibulo. Mudabwa kwambi-ri kuona kukwaniritsidwa kwake.

� Maulosi ena ndi okhudza uthenga wochokera kwa Mulunguwonena zimene zichitike m’tsogolo.

03

Kodi MuyeneraKukhulupirira Baibulo?

11

Page 12: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

F U F U Z A N I M O Z A M A

Onani kugwirizana pakati pa sayansi yamakono ndi Baibulo, ndipo fufuzani maulosiena a m’Baibulo ochititsa chidwi.

4. Baibulo ndi lolondolapa nkhani za sayansiKale anthu ankakhulupirira kuti dzikoli lakhazikika pachinthuchinachake. Onerani VIDIYO.

Ndiyeno onani zimene zinalembedwa m’buku la Yobu zaka 3,500zapitazo.Werengani Yobu 26:7, kenako mukambirane funso ili:

˙ N’chifukwa chiyani mfundo yakuti dzikoli lili “m’malere” ndiyodabwitsa?

Cha m’ma 1800 m’pamene anthu anazindikira za kayendedwe ka madzi.Koma taonani zimene Baibulo linanena zaka pafupifupi 3,500 zapitazo.Werengani Yobu 36:27, 28, kenako mukambirane mafunso awa:

˙ N’chifukwa chiyani kufotokoza za kayendedwe ka madzi m’njirayosavuta chonchi n’kochititsa chidwi?

˙ Kodi malemba amene mwawerengawa akuthandizani kukhulupiriraBaibulo?

5. Baibulo linaneneratu nkhanizofunika kwambiriWerengani Yesaya 44:27–45:2, kenako mukambirane funso ili:

˙ Kodi Baibulo linaneneratu za chiyani kutatsala zaka 200 kutiufumu wa Babulo ugonjetsedwe?

Onerani VIDIYO.

VIDIYO: Dziko Silikhala Pachilichonse(1:13)

VIDIYO: Baibulo LinaneneratuKuti Mzinda wa BabuloUdzagonjetsedwa (0:58)

(

(

Baibulo limafotokoza zakayendedwe ka madzi

Page 13: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

Olemba mbiri anatsimikizira kuti Mfumu Koresi ya Perisiya, inago-njetsa mzinda wa Babulo mu 539 B.C.E.� Iye ndi asilikali ake ana-patutsa madzi a mumtsinje umene unkateteza mzindawo. Kenakoanapeza mageti osatseka n’kulanda mzindawo popanda kumenyankhondo. Panopa, padutsa zaka 2,500 chigonjetsereni Babulo,koma pamalo pamene panali mzindawu sipanamangidwe chilicho-nse mpaka pano. Taonani zimene Baibulo linaneneratu.

Werengani Yesaya 13:19, 20, kenako mukambirane funso ili:

˙ Kodi zimene zinachitika ku Babulo zimasonyeza bwanji kutiulosiwu unakwaniritsidwa?

� B.C.E. imaimira “Before the Common Era,” kutanthauza nthawi yathu isanafike,ndipo C.E. imaimira “Common Era,” kutanthauza nthawi yathu ino.

6. Baibulo linaneneratu zimenezikuchitika masiku anoBaibulo limasonyeza kuti masiku ano, ndi “masikuotsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) Taonani zimene Baibulolinaneneratu zokhudza masiku ano:

Werengani Mateyu 24:6, 7, kenako mukambiranefunso ili:

˙ Kodi Baibulo linaneneratu kuti masiku otsirizakudzachitika zotani?

Werengani 2 Timoteyo 3:1-5, kenako mukambiranemafunso otsatirawa:

˙ Kodi Baibulo linaneneratu kuti anthuambiri adzakhala otani?

˙ Kodi ndi makhalidwe ati amene inuyomwaonapo?

ZIMENE ENA AMANENA: “Baibulo ndi buku la nkhani zongopeka basi.”

˙ Kodi inuyo muli ndi umboni wotani wotsimikizira kuti Baibulo ndi lodalirika?

Malo amene panali mzindawa Babulo ku Iraq

13

Page 14: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

ZOMWE TAPHUNZIRAMbiri yakale, sayansi komansomaulosi zimasonyeza kuti Baibulondi lodalirika.

Kubwereza˙ Kodi zimene Baibulo limanenandi zoona kapena n’zongopeka?

˙ Kodi Baibulo ndi lolondola pankhani ziti zokhudza sayansi?

˙ Kodi inuyo mumaona kutiBaibulo limalosera zam’tsogolo?N’chifukwa chiyani mukutero?

Tsiku limene tamaliza phunziroli

ZolingaN Kuti muzikhulupirira kwambiri

Baibulo, werengani kapenaonerani zimene zasonyezedwapakamutu kakuti OnaniZinanso.

N Zina:

O N A N I Z I N A N S O

Kodi Baibulo limatsutsana ndizimene asayansi amanena?“Kodi Sayansi ImagwirizanaNdi Baibulo?” (Nkhani yapawe-busaiti)

Kodi ndi zinthu ziti zomwetiyenera kudziwa pa nkhaniya “masiku otsiriza”?“Maulosi 6 a M’BaibuloAmene AkukwaniritsidwaMasiku Ano” (Nsanja ya Olonda,May 1, 2011)

Kodi ulosi wa m’Baibulowonena za Ufumu wa Girisiunakwaniritsidwa bwanji?“Mawu a Ulosi Amatilimbiki-tsa”

( 5:22

Kodi maulosi a m’Baibulo ana-thandiza bwanji munthu winakusintha mmene ankaoneraBaibulo?“Ndinkaona Kuti KulibeMulungu” (Nsanja ya OlondaNa. 5 2017)

Kuti mupeze mavidiyo ndi zinthu zina zogwiritsa ntchito muPHUNZIRO 03, pangani sikani kachidindo aka kapena tsegulanibuku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale pa jw.org

Page 15: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

MUNGAKHALE ND I MOYOMPAKA KALEKALE

K U P H U N Z I R A B A I B U L O M O K A M B I R A N A

Printed by WatchTower Bible andTract Society of South Africa NPC1 Robert Broom Drive East,Rangeview, Krugersdorp, 1739, R.S.A.Made in the Republic of South AfricaLopangidwa ku Republic of South Africa

Kodi mungakonde kudziwa zambiri zimeneBaibulo limaphunzitsa?

Iyi ndi mbali yochepa chabe ya zimene munga-phunzire m’buku la Mungakhale Ndi Moyo MpakaKalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana.

Palibe amene adzakuuzeni kuti mugule bukulikapenanso kuti mulipire kuti muziphunzira.Tidzasangalala kuphunzira nanu pa nthawindi malo amene mungasankhe.

Mukamaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchitobukuli muphunzira nkhani zambiri kuphatikizapo:

N Cholinga cha moyoN Zimene mungachite kuti mupeze

mtendere weniweniN Zimene mabanja angachite kuti

azisangalalaN Zimene Baibulo limalonjeza zokhudza

m’tsogolo

Kodi mwasangalala ndi zimenemwaphunzira?

Kuti mupeze bukuli komanso kutimupitirize kuphunzira Baibulo, pemphaniwa Mboni za Yehova aliyense kapenansolembani fomu yopempha phunziro laBaibulo kudzera pa jw.org.

Photo Credit: Page 13, Babylon’s ruins:Image ˘ Homo Cosmicos/ShutterstockKabukuka sitigulitsa. Timapereka ngati njiraimodzi yophunzitsira anthu Baibulo padzikolonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyindi zimene anthu amapereka mwa kufunakwawo. Ngati mukufuna kupereka ndalama,pitani pa donate.jw.org.Malemba onse m’kabukuka akuchokera muBaibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatu-lika, kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina.

Malifalensi onse amene ali m’kabukuka ndiofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova.Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Yambani Kuphunzira BaibuloEnjoy Life Forever!—Introductory Bible LessonsKosindikizidwa mu January 2021Chichewa (lffi-CN)˘ 2021WATCH TOWER BIBLE AND TRACT SOCIETYOF PENNSYLVANIA

Ofalitsa

Page 16: MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

lffi-C

N2

10

20

5

Kodi n’zothekakukhala ndi moyompaka kalekale?

Kodi mungayankhe kuti . . .˙ inde?˙ ayi?˙ mwina?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Olungama adzalandira dziko lapansi,ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—SALIMO 37:29.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?

M’tsogolomu mudzakhala ndi moyowosangalala komanso wamtenderelimodzi ndi banja lanu ndiponso anzanu.—YEREMIYA 29:11.

Mudzasangalala ndi moyo osati kwa nthawiyochepa koma kwamuyaya.—SALIMO 22:26.

KODI TIYENERA KUKHULUPIRIRA BAIBULO?

Inde. Kuti mudziwe chifukwa chake onanimaumboni omwe akupezeka m’maphunziroatatu amene ali m’kabukuka. Mitu yakendi iyi:

Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?Baibulo Limatithandiza Kukhala NdiChiyembekezoKodi Muyenera Kukhulupirira Baibulo? s