22
MMODZI P A M ILIONI Zikomo inu, m’bale. Zikomo inu, M’bale Shakarian. Ndipo mmawa wabwino, abwenzi. Ndithudi nzabwino kukhala tiri pano mu Los Angeles kachiwiri mmawa uno, patsogolo pa msonkhano waukulu uwu, ndi kudza kwa msonkhano wa sabata ikudza iyi uko ku Embassy Hotel. Ine ndikuyembekeza kukakuonani inu nonse kumeneko. Ndipo tonse tiri pansi pa kuyembekezera kwakukulu kuti tikakomane ndi Ambuye wathu Yesu, kukamuwona Iye kumeneko. Iye analonjeza kuti Iye akanati azikhalapo. “Kulikonse komwe awiri kapena atatu anali atasonkhana palimodzi,” Iye akanakhala ali kumeneko. 2 Ndipo ine ndikutsimikiza kuti ine ndinakomana naye Iye mmawa uno pamene ine ndimakwera masitepe a mu nyumba yoyankhuliramo iyi kuno, pamene anthu onse ndi kuyembekezera kwakukulu, amayembekezera kadzutsa ndi kumayankhula. Ndipo nzabwino kuti ndasonkhana pano ndi inu, ndi kwa omvetsera apa wailesi. Alipo ochuluka kwambiri muno, iwo ali…ine ndinachita kupita mpaka kuzipinda zina zosanjikiza, ndi kukayankhula kwa ochepa. Ndipo ndawona zopempha zochuluka kwambiri, vuto la mtima, ndi matenda osiyana a mmatupi awo, ndipo ife tiri pano tsopano kuti tiwapempherere odwala ndi osautsika. 3 Basi pamene ine ndimafika pamwamba pa masitepe…Ine ndikuyang’ana pa njonda yachikulire tsopano. Iye anabwera apo kwa ine, ndipo anati, “M’bale Branham, zaka zapitazo…” Iye anati iye anali ndi vuto la mtima moyipa kwambiri moti iye… iwo ankaganiza kuti iye akanati afe. Ndipo ndinali ndi pemphero pa iye, ndipo chisomo cha Mulungu chinamuchiza iye. Ndipo ali pano mmawa uno, atadutsa mu ma eyite ake, akungosangalala. Kotero izo zikutipangitsa ife kutenga kugwira kwatsopano. 4 Ndipo tsopano ine ndithudi ndikupempha mapemphero a anthu uko mu dziko la wailesi, chimodzimodzinso pano. Ndikachoka ku msokhano uno, ine ndikupita ku Ulaya, mpaka uko mu Afrika ndi kozungulira, pa misonkhano. Ndipo uku ndi kupita mwa masomphenya, kotero ukakhala msonkhano waukulu kumeneko, ine ndikutsimikiza. Ndipo ine ndamverera kwa zaka kuti Ambuye akhala akufuna kuti ine ndibwerereko. Utumiki waung’ono wodzichepetsa, wonyozeka umene Iye anandipatsa ine, ine sindikuganiza kuti Iye wathana nawo kwenikweni iwo panobe, kumeneko. Zikuwoneka ngati pakhoza kukhala pali moyo kwinakwake umene ine ndingakhoze kukawugwira mu khoka la Uthenga, limene Iye anandipatsa ine kuti ndizisodzera nalo anthu, njira ya

CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

  • Upload
    others

  • View
    4

  • Download
    0

Embed Size (px)

Citation preview

Page 1: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

MMODZI PA MILIONI

Zikomo inu, m’bale. Zikomo inu,M’bale Shakarian.

Ndipo mmawa wabwino, abwenzi. Ndithudi nzabwinokukhala tiri pano mu Los Angeles kachiwiri mmawa uno,patsogolo pa msonkhano waukulu uwu, ndi kudza kwamsonkhano wa sabata ikudza iyi uko ku Embassy Hotel. Inendikuyembekeza kukakuonani inu nonse kumeneko. Ndipotonse tiri pansi pa kuyembekezera kwakukulu kuti tikakomanendi Ambuye wathu Yesu, kukamuwona Iye kumeneko. Iyeanalonjeza kuti Iye akanati azikhalapo. “Kulikonse komweawiri kapena atatu anali atasonkhana palimodzi,” Iyeakanakhala ali kumeneko.2 Ndipo ine ndikutsimikiza kuti ine ndinakomana nayeIye mmawa uno pamene ine ndimakwera masitepe a munyumba yoyankhuliramo iyi kuno, pamene anthu onse ndikuyembekezera kwakukulu, amayembekezera kadzutsa ndikumayankhula. Ndipo nzabwino kuti ndasonkhana pano ndiinu, ndi kwa omvetsera apa wailesi. Alipo ochuluka kwambirimuno, iwo ali…ine ndinachita kupita mpaka kuzipinda zinazosanjikiza, ndi kukayankhula kwa ochepa. Ndipo ndawonazopempha zochuluka kwambiri, vuto la mtima, ndi matendaosiyana a mmatupi awo, ndipo ife tiri pano tsopano kutitiwapempherere odwala ndi osautsika.3 Basi pamene ine ndimafika pamwamba pa masitepe…Inendikuyang’ana pa njonda yachikulire tsopano. Iye anabwera apokwa ine, ndipo anati, “M’bale Branham, zaka zapitazo…” Iyeanati iye anali ndi vuto la mtima moyipa kwambiri moti iye…iwo ankaganiza kuti iye akanati afe. Ndipo ndinali ndi pempheropa iye, ndipo chisomo cha Mulungu chinamuchiza iye. Ndipo alipano mmawa uno, atadutsa mu ma eyite ake, akungosangalala.Kotero izo zikutipangitsa ife kutenga kugwira kwatsopano.4 Ndipo tsopano ine ndithudi ndikupempha mapempheroa anthu uko mu dziko la wailesi, chimodzimodzinso pano.Ndikachoka ku msokhano uno, ine ndikupita ku Ulaya,mpaka uko mu Afrika ndi kozungulira, pa misonkhano.Ndipo uku ndi kupita mwa masomphenya, kotero ukakhalamsonkhano waukulu kumeneko, ine ndikutsimikiza. Ndipoine ndamverera kwa zaka kuti Ambuye akhala akufunakuti ine ndibwerereko. Utumiki waung’ono wodzichepetsa,wonyozeka umene Iye anandipatsa ine, ine sindikuganizakuti Iye wathana nawo kwenikweni iwo panobe, kumeneko.Zikuwoneka ngati pakhoza kukhala pali moyo kwinakwakeumene ine ndingakhoze kukawugwira mu khoka la Uthenga,limene Iye anandipatsa ine kuti ndizisodzera nalo anthu, njira ya

Page 2: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

2 MAWU OLANKHULIDWA

mwamachiritso Auzimu, kupempherera odwala. Ndipo ndithudiine ndikupempha mapemphero anu, nonse anthu inu pano ndiiwo omwe ali kunja mwa omvetsera pa wailesi.5 Tsopano ine ndiribe nthawi basi kuti nditenge nkhani ndikulalikirapo, chimene ine ndikuyembekezera kutero akathamaminiti pang’ono kuno m—mu…nyumba yoyankhuliramoino, koma kungoti ndiyankhule n—ndi inu mphindi pang’ono,kuti tidziwane. Ndipo kwa anthu kunja mu dziko, ine ndikutindipemphe pemphero kwa iwo akunja uko, pakali pano,ndi mkati muno nanunso. Ndipo ndithudi ndine wokondwakukomana nao abwenzi abwino onse atsopano awa omwe inesindinayambe ndakomana nawo kale, ndangofika pokomananawo iwo mmawa uno.6 Ife takhala tiri ndi nthawi zazikulu mu misonkhano mumalo enawa. Ine sindikumapita kunja mochuluka kwambiripanonso, ndi zotangwanitsa kwambiri. Ife tikungoyesa kukhalatikuutenthetsa mseu wa pakati pa Jeffersonville, Indiana ndiTucson, Arizona, komwe ife tinasamukirako uko zaka zingapozapitazo, mwa masomphenya a Ambuye, omwe anatitumiza ifeuko, aponso, ndisakudziwa komwe ine ndinali kupita. Ndipoambiri a inu kuno, ku Clifton, ine ndinayankhula kwa inupang’ono izo zisanachitike mu msonkhano wa ku Phoenix, zamasomphenya omwe anabwera. Ine ndinawaona Angelo asanundi awiri mu kuundana.7 Ndipo ine ndikudziwa, kwa omvetsera pa wailesi,mwinamwake ambiri a inu sindinu a Uthenga wathunthu, ndipoizi zikhoza kuwoneka zododometsa pang’ono kwa inu. Chomwe,izo zikanati zitero kwa ine, koma pali…Aliyense yemweangakhoze kulongosola chirichonse, inu simumasowa kutimuchite kuzilandira izo aponso mwa chikhulupiriro. Ndi zinthuzomwe ife sitingakhoze kuzilongosola, nzomwe ife timayenerakuti tizizilandira mwa chikhulupiriro. Ife sitingakhozekumulongosola Mulungu. Palibe munthu yemwe angakhozekumulongosola Mulungu. Iye ndi wochita mwayekha, ndipo Iyendi wamkulu ndi wamphamvu. Ife basi—ife timangovomerezaizo chifukwa kuti ife timadziwa kuti Iye alipo. Ndiyeno mwachikhulupiriro chathu, pa kulandira izo, Iye amabweretsayankhommbuyo kwa ife, ubatizo waMzimuWoyera.8 Chimene, ine nditi ndiyankhule kwa inu pa izo, mumphindi zochepa pano, pa, “Njira ya Mulungu, kapena maloopembedzerapo.” Ndipo malo okha omwe inu mungakhozekumupembedzapo Iye, malo okha omwe Iye angati akomanenanu konse, payenera kukhala…Pali Mpingo umodzi, maloamodzi, nthawi imodzi, anthu amodzi, mwa onse omweMulunguamakomana nao. Ndipo ine ndikuyembekeza kuti Ambuyeadalitsira Uthengawo kumitima yanu pano.9 Tsopano, kubwera ku Tucson, izo zinali zachilendo,masomphenya awo poyankhula kwa inu mu Dzina la Ambuye.

Page 3: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

MMODZI PA MILIONI 3

Palibe amodzi a iwo monga ine ndikukumbukira konse, mutatimumufunse wina aliyense ngati iwo angakhoze kukumbukiranthawi iliyonse, yomwe Iye anayamba wanenapo chirichonsekupatula chomwe chinali Choona. Izo nthawizonse zimachitikabasi momwe Iye wanenera kuti izo zidzachitikira.

10 Ndipo Iye akuyenera kumatero, molingana ndi Malemba,kubwerera kwa ife mu masiku otsiriza ano, mu utumiki wamtundu uwu. Izo zidzakhala ukadzachitika ubatizo wa Mzimu,ndi kuyankhula mu malirime, ndi machiritso Auzimu, ndizina zotero, zinthu izi. Kuyika chapamwamba pa uthenga wachipentekoste ndi chomwe ife tikuchikamba lero. Utumiki uwuwa Khristu Mwiniwake akutsanziridwa pakati pa anthu Ake,ndi zinthu zofanana zomwezo zimene Iye ankachita pamene Iyeanali pa dziko lapansi pano; mu Thupi Lake, Mkwatibwi, yemweali gawo la Iye, akuchita zinthu zomwezo, monga Mwamunandi Mkazake, kapena Mfumu ndi Mfumukazi, basi usanachitikemwambo wa Chikwati.

11 Sabata ino, Ambuye akalola, ine ndikukhumba kutindidzayankhule zina pa zimenezo, uko ku msonkhanowathu wokopa anthu kuno, ku—Embassy Hotel, ndikukhala ngati mudziwane nayo njira yanga yodzichepetsayochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,ngati munthu sadziwa njira yoti apite nayo, zoti achitekapena momwe angatembenukire, i—iwe suli kuyenda mwachikhulupiriro aponso; iwe ukungolingalira, iwe ukupenekera.Ndipo kupenekera ndi k—ku “kupita patsogolo popandaulamuliro wovomerezeka.” Kotero ngati ife tiribe ulamuliroweniweni wovomerezeka kuti tizidziwa zomwe Mulungu anatizikanadzachitika mu ora lathu, kodi ife tikomana nalo chotaniora lino? Ndipo ife tiyenera kuti tikomane nalo, tikudziwa, mwachikhulupiriro mu Mawu Ake, zinthu zomwe zikuyenera kutizizichitika tsopano; ndi chikhalidwe cha mafuko, chikhalidwecha anthu, chikhalidwe champingo, ndi zina zotero.

12 Ife tiyenera kuti tizizidziwa zimenezo, ndiyeno momwetingayendere kuti tikomane nazo izo. Ngati iwe sudziwamomwe ungachitire izo, iwe basi—basi zomwe ife tinkakondakuzitcha, za mtundu wa, mwachisawawa; kungodumphiramo,ukuyembekeza kuti zikhala pano, kuyembekeza ichi ndikuyembekeza icho, ndi “kodi zitero?” Koma Mulungu samafunakuti ife tizichita izo. Iye amafuna kuti ife tizidziwa zomweIye ananena zokhudza tsiku lino, ndiyeno tizikomana nazo izomwa chikhulupiriro, chifukwa Iye anati izo zikanati zidzakhalemwanjira imeneyo. Ndiye ife—ife tidziwa kuti ndinu Owonandiye, chifukwa inu mulibe mawu a munthu wina pa izo; inumuli ndi Mawu Ake a zomwe ife tiyenera tizichita. Ndipo ifetikuyembekeza kuti Atate athu Akumwamba a—apereka izi kwaife sabata lino.

Page 4: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

4 MAWU OLANKHULIDWA

13 Tsopano, ine ndikupepesa kuti ine ndinadukiza, pa zomweine ndimanena mphindi zingapo zapitazo, za kubwera kuTucson. Ndipo ine ndinkaganiza, mwiniwanga, kuti awoanali mathero a moyo wanga. Ine ndinkaganiza palibe winaakanakhoza nkomwe kupirira nako kugwedeza uko kwachikhalidwe icho chomwe chinachitika mu masomphenya ajammawa uwo, pafupi teni koloko kwathu, yemwe akanakhozankomwe kukhala moyo zitachitika izo. Moti, ine ndinabweraku Tucson, kupanga zokonzekera ndi mwana wanga, za mkaziwanga n—ndi ana kuti adzapite ndi iye ine ndikadzakhalanditapita, chifukwa ine ndinkaganiza awo anali mathero anga.Ndipo ine, mu Phoenix ndi mwambiri mu misonkhano izozisanachitike, ine ndinakuuzani inu basi momwe izo zikanatizidzachitikire.14 Chabwino, miyezi pang’ono pambuyo pake, ine ndinaliuko mu Sabino Canyon mmawa wina, komwe kuli kumpotochabe kwa Tucson. Ine ndinali ndiri uko kukapemphera. Ndipopamene ine ndinali kupemphera, ine ndinali ndi dzanja langanditalikweza mmalere, ndikuti, “Atate, ine ndikukupemphaniInu kuti Inu mwanjira ina mundithandize ine, ndipatseni inemphamvu, za kwa ora lomwe ine tsopano ndikukomana nalo.Ndipo ngati ntchito yanga yatha kuno pa dziko lapansi, ndiyeine ndiyenera kuti ndibwere kwa Inu. Ndipo izo si kuti inendikudandaula nako kubwerako, koma ine ndikudziwa kutiInu mulisamalira banja langa. Ndipo i—ine ndikungopemphanyonga zofunika pa ora ili.” Ndipo chinachake chinakhudzadzanja langa!15 Tsopano, omvetsera pa wailesi, izi zikhoza kuwonekazachilendo zomwe ndanenazi, koma ndi zoona. Ndipo Mulungundi Woweruza wanga.16 Ine ndinayang’ana mu dzanja langa, ndipo umo munalilupanga, linali ndi chotetezera ku gawo la chigwiriro. Ndipochigwirirocho pachokha chinali chopangidwa ndi ngale, ndipobasi chinkangowoneka monga mwa mtundu wonga wa golideku gawo la chigwiriro. Ndipo—mpeniwo pawokha unkawonekangati iwo unali monyezimirirapo, o, chinachake chonga kromukapena chinachake chikunyezimira mu dzuwa.17 Tsopano, apo inali pafupi teni kapena leveni koloko mmawa,pamwamba pomwe pa phiri. Inu mukhoza kulingalira momwemunthu (yemwe ine ndikumverera kuti ndiri mu malingaliroolondola) akanati amverere ataima apo ndi lupanga lopandakochokera, anthu ali kutali mailosi ndi mailosi, ukuligwirizirailo mu dzanja lako. Ine ndinalimverera ilo, ndinalitenga ndipondinaugwedeza mpeniwo mmbuyo ndi mtsogolo, ndipo, bwanji,ilo linali lupanga.18 Ndipo ine ndinayangana pozungulira. Ine ndinati,“Chabwino, tsopano, izo zikanakhoza kuchitika motaninkomwe? Pano ine ndiri nditaima pano, apa, pomwe, ndipo

Page 5: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

MMODZI PA MILIONI 5

palibe aliyense alipo kwa mamailosi ndi mamailosi, ndipokodi ilo lachokera kuti?” Ndipo ine ndinati, “Chabwino, i—ine ndikulingalira mwinamwake ndi—Ambuye akundiuza inekuti ndi nthawi yanga yothera.”

Ndipo Liwu linayankhula ndipo linati, “Ili ndi Lupanga laAmbuye.”19 Ndipo ine ndinaganiza, “Chabwino, lupanga, ndiye ndila monga mfumu, kwa wonyamula lupanga.” Inu mukudziwa,momwe zinkachitikira mu England ndi ku malo osiyana. Inendinaganiza, “Icho ndi chomwe ili ntchito yake, kwawonyamulalupanga.” Ndipo ine ndinaganiza, “Chabwino, mwinamwakeine ndikuyenera kuti ndizikayika manja pa anthu, kapena…”Ine ndinali ndi mitundu yonse…Malingaliro aumunthu akhozakukhala atasokonezeka onse, inu mukudziwa. Iwe sumadziwa.Malingaliro athu ndi amalire; Ake ndi opandamalire. Kotero,ndipo pamene ine ndinali, izo…Ndiye ilo linachoka mdzanjalanga ndipo ine sindinadziwe komwe ilo linapita, linangosowa.Bwanji, ngati munthu sakanakhoza kumvetsa pang’ono pokhapa zinthu zauzimu, i—iwe ukanakhoza kupenga monga choncho.Iwe ukanakhala utaima apo, ndi kumadabwa zomwe zachitika.20 Ndipo Iye anati, “Masomphenyawo si kutha kwa nthawiyako. Iwo ndi a utumiki wako. Lupanga ilo ndilo Mawu.Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri zitsegulidwa, zinsinsi za…”21 Ndiyeno masabata awiri zitachitika izo, kapena miyeziiwiri, kani, zitachitika izo, ine ndinali uko mu phiri ndigulu la amzanga pamene izo, zinachitika. Angelo asanundi awiri, owoneka bwino basi monga inu mwaimira apa,anabwera akusesa pansi kuchokera Kumwamba. Miyala mumapiri inagudubuzika ndi kutsika nalo mapiri, n—ndipo anthuomwe anali ataima pamenepo anali akukuwa ndi kumapitiriza,inu mukudziwa, ndipo fumbi likuwuluka ponseponse. Ndipopamene izo zinatero, Iye anati, “Bwerera kwanu. Tsopanozikakhala kuti, Mngelo aliyense akakhala ali chimodzi chazisindikizo za Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri.”22 Zomwe, ziri pa tepi. Ndipo bukhulo litulutsidwaposakhalitsa kwambiri, pokhala kuti tsopano likukonzedwagalamala. Monga inu mukudziwira, galamala yanga si yabwinokwambiri, ndipo anthu sakanati…Inu mukuyenera kukhalaanthu omwe mumandikonda ine ndi kumadziwa momwemungamandimvetsere ine pa galamala yanga. Koma wafiorojewina akundikonzera ine galamalayo, ndipo akuchotsamo zonseza a—a…Chabwino, mwinamwake ine ndinanena mawuolakwika pamenepo. Ine sindikudziwa nkomwe. Kotero, inendinamumva wina akuseka, kotero ine ndikulingalira kuti“galamala” si yolondola. Koma monga bambo wa chi Dutch,inu muzinditenga ine pa zomwe ine ndikutanthauza ndipo osatizomwe ine ndikunena, mwinamwake.

Page 6: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

6 MAWU OLANKHULIDWA

23 Ndipo ndi maminiti atatu okha tsopano, ine ndauzidwa, kutitifike potseka pa purogramu.24 Tsopano, inu anthu okondedwa uko mu dziko la wailesi,ndi inu omwe muli odwala ndi osowa muno mwa omvetsera,kodi inu mungangoikana manja pa wina ndi mzake tsopanopamene ife tikukhala ndi mawu awa a pemphero kwa odwala.Tsopano, Yesu anati, utumiki Wake wotsiriza kwa Mpingo,“Zizindikiro izi zidzawatsatira iwo omwe akhulupirira.” “Iwo,”iwo omwe akhulupirira! “Ngati iwo aika manja awo pa odwala,iwo adzachira.”25 Wokondedwa Atate Akumwamba, ife tiri ngati ana lero,ife tikumvera zomwe Inu munati tizichita. Ife tikuyika manjapa zopempha zonse za pa lamya izi. Inu mukuwaona iwo ukomu dzikoli kunja uko, momwe iwo aliri osowa, akuvutika.Inu mukuwaona iwo pano omwe ali osowa, akuvutika. Ndipoife tikuwapereka iwo kwa Inu, Mulungu Wokondedwa, ndichikhulupiriro ichi mu Mawu Anu momwe Inu munati,“Zizindikiro izi zidzawatsatira iwo omwe akhulupirira. Ngatiiwo aika manja awo pa odwala, iwo adzachira.” Perekaniizi, Ambuye, mu Dzina la Yesu Khristu. Ameni. [Maloosajambulidwa pa tepi—Mkonzi.]

[M’bale Branham akutsirizitsa kuulutsa koyamba kwa pawailesi—Mkonzi.]

✩ ✩ ✩ ✩ ✩ ✩ ✩26 Zikomo inu, M’bale Shakarian. Ndithudi ndi mwayiwaukulu kubwerera kachiwiri pa kuulutsaku, kutindidzayankhule kwa ena a abwenzi anga uko mu dziko lawailesi, chimodzimodzi ndi omwe ali pano.27 Ndipo ndithudi ife tikufikitsira kuitanira uku kwainu, kuti mubwere ku Embassy Hotel mawa madzulo,kuti mudzapemphereredwe. Ndipo osati izo zokha, komamuwabweretse iwo omwe ali ochimwa ndi iwo omwe aliobwerera mmbuyo. Ngati ife titi tidzangokhala ndi pemphero paodwala, ndipo ife timamuwona Mulungu mosalekeza akuchitazozizwitsa zazikulu, koma izo ndi zachiwiri. Chinthu chachikulundi kuti upulumutsidwe, kudzazidwa ndi Mzimu wa Mulungu,zomwe ine nditi ndiyankhule kwa inu pafupi mu mphindizochepa zokha pano, ndi kukwanira kwa momwe ife tiyenerakukhala odzazidwa ndi MzimuwaMulungu.28 Ndipo machiritso Auzimu kawirikawiri amakopa chidwikwa anthu, ndi kuwabweretsa iwo mu Kukhalapo kwaMulungu. Pamene Mulungu akuchita chinachake chi—chimeneiwo amadziwa kuti ndi-…chabwino, izo sizimamvetsedwaayi. Ife sitingakhoze kusonyeza mwakachitidwe momwe izozimachitikira. Mulungu amachita izo mwa njira Yake Yomweyaikulu. Ndiye izo zimakopa tcheru cha anthu, podziwa kutikulipo Kukhalapo kwa Mphamvu penapake, yomwe ingakhoze

Page 7: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

MMODZI PA MILIONI 7

kuchita chinachake chomwe chiri chopitirira kumvetsa kwaumunthu, ndipo izo zimawapangitsa iwo kuti aziyang’ana kwaMwanawankhosa wa Mulungu. Ndipo nthawizonse, machiritsoAuzimu; ine ndimauzidwa, ndipo ine ndikukhulupirira,mwiniwanga, kuti pafupi pakati pa sikisite, mwinamwake, ndimagawo sevente pa zana, a utumiki wa Ambuye wathu, analipa machiritso Auzimu. Ndipo Iye ankachita izo kuti awakopeanthu. Ndiye pamene iwo anali apo, Iye anati, “Kupatula inumutakhulupirira kuti Ine ndine Iye, inu mudzawonongeka mutchimo lanu.”29 Tsopano, machiritso Auzimu ndi khadi lalikulu lokokera,kuti uwafikitsire anthu poyang’ana kwa Ambuye Yesu. NdipoDoctor F.F. Bosworth, yemwe ambiri a inu, munali abwenzi ake,ndipo munkamudziwa iye, ndipo utumiki wake unatanthauzamochuluka kwambiri kwa ine ndiri mtumiki wamng’ono.Ine ndinayamba kupita mu misonkhano yanga, ndipo inendinakomana ndi M’bale Bosworth. Iye ankakonda kunenakuti, “Machiritso Auzimu,” ndi kuyankhula kwakung’ono kwakhambi tsopano, iye ankati, “Machiritso Auzimu ndi nyambopa mbeza ya nsomba.” Anati, “Inu simumaisonyeza nsombambeza. Inu mumaisonyeza iyo nyambo, ndiyeno iyo imatsatiranyambo yomwe ili pa mbezayo.” Kotero ndi chimene ifetikuyesera kuchita. Ndicho chathu…ife…Cholinga chathu ndikuti tiwatengere anthu kwa Ambuye Yesu Khristu. Ndipo Iye aliyemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse. Kotero ngati Iye analiMchiritsi mumasiku apitawo, Iye ali Mchiritsi lero.30 Umboni wandekha basi ine ndisanati ndiwapempherereodwala uko mu dziko la wailesi. Anali masiku angapo apitawo,ine ndinali nditakhala mu mapiri komwe chinthu chachikuluchinali chitachitika pamaso pa abale khumi ndi asanu kapenamakumi awiri mmenemo, komwe Mngelo wa Ambuye anabweramotsika kwambiri, ndipo Kuwala kwakukulu kukuuluka ngatinyenyezi, kunaphulitsa pozungulira mu mapiriwo, ndipo miyalaikuwuluka kwa mapazi mazana awiri, kapena kuposa, kudutsapa malowo, ikudula nsonga za mitengo. Ndipo ine ndinalinditaima pansi pa Iko komwe. Ndipo ine ndinawauza iwomphindi zingapo zokha izo zisanachitike, Zikanakhala ziripouko ndi zomwe zikanati zichitike; moona, izo zinanenedwadzulo lake. Ndipo amuna onse awa akuthamangira pansipa magalimoto ndi chirichonse, poyesera kuti athawe. Iwosankadziwa chifukwa chomwe izo zinali kuchitika. NdipoIye anayankhula ndipo ananena zomwe zikanati zidzachitikemwamsanga kumene pambuyo pake.31 Nditakhala pa mwala wina uwo apo, apo pomwe pamene Iyeanali atawonekera, ine ndinali ndi n—mzanga yemwe anali ndiife, yemwe anali atabwera uko kuchokera ku Minnesota. Abaleake ali pano mmawa uno ndipo ine sindikutsimikiza koma kutiiye akhoza kukhala ali pano mu zipinda zapamwamba zinazi.

Page 8: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

8 MAWU OLANKHULIDWA

Iye anali DonavonWeerts, ndimnyamatawabwino, waChiluterayemwe anali atangopereka moyo wake kwa Khristu ndipo analiatadzazidwa ndi Mzimu. Mnyamata wodzichepetsa kwambiriwachi German, pafupi usinkhu wa zaka sate, banja, ana awirikapena atatu aang’ono. Iye anasamukira uko ku Tucson kungotiadzakhale oyandikana ndi ife, komwe firii kapena foro handiredianasamukirako kuti akakhale oyandikana nawo.Kotero iye…32 Ndipo ndine wokondwa kuti ndiri nawo oyandikana nawochoterowo. Iwo amanditsatira ine ulendo wonse kuchokera kuSouth Africa, ndi kulikonse amakhalapo, basi kuti azikhalapafupi ndi kumawona…ali nane, ndi kuti azikhala ndi ine ndikumakondwera nazo zisangalatso za Ambuye.

Munthu wodzichepetsa choteroyo, ine sindinalikumuzindikira konse iye mochuluka kwambiri.33 Ndithudi, anthu omwe ine ndimawadziwa ndi kuyanjananawo amakhala ngati m’bale wanga yemwe, mlongo. Inendimawapenya iwo, ndi kumverera ngati ine ndikuganizakuti iwo akuchoka pa mzere, ndi kuwatengera iwo kumbaliimodzi ndi kuyankhula nao, chifukwa ine ndimawakonda iwo.Ife tikufuna kuti tidzakakhale ku Ulemerero limodzi. Ndiponthawizina mwinamwake, mu misonkhano, inu mumaganizakuti ndimayankhula mwaukali kwa inu. Izo si zochokera apo.Izo siziri chifukwa chakuti ine sindimakukondani inu, komaizo zimabwera kuchokera mu mtima mwanga, chifukwa i—ine…Izo ziyenera kuti zizikhala mwanjira imodzi yokha. Iliponjira imodzi yokha yoti uzimutumikira nayo Mulungu, ndipondiyo…Ndipo ife tiyenera kumakhala mu njira Yake, ziribekanthu chomwemaganizo athu ali. Njira Yake!34 Ndipo ine ndinazindikira Donavon, pa nsonga yakumanjaya khutu lake, inali yotupa mwina nthawi zitatu makulidweake, ndipo linkawoneka lofiira kwambiri. Chabwino, tsopanopoganiza mwinamwake pokhala kuti anali uko mu chipululukwa masiku angapo, komwe ife tinakhala tiri, kuti mwina iyeanali atabaidwa ndi kaloga mu khutu lake. Koma, nditaligwiradzanja lake, ine ndinapeza kuti iyo inali khansara. Koteroine ndinati kwa Donavon, ine ndinati, “Donavon, kodi iwe…Kodi izo zakhala ziri motalika bwanji pa khutu lako?”Kungokhala ngati kumuponyera iye kumbali, ngati kuti inesindimadziwa. Ine ndinati, “Ndi utali wotaniwomwe izo zakhalaziri pamenepo, Donavon?”

Iye anati, “M’bale Branham, pafupi miyezi sikisi,” iyeanatero.

Ine ndinati, “Bwanji iwe sunazinene izo kwa ine?”35 Iye anati, “O, pokuwonani inu otangwanika kwambiri,”anati, “Ine sindimafuna k—kuti ndichite izo.” Anati,“Ine ndimangoganiza mwinamwake nthawiyina Ambuyeakanakuuzani inu.”

Page 9: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

MMODZI PA MILIONI 9

Kotero ine ndinati, “Kodi iwe ukuzindikira chomwe ichochiri?”

Iye anati, “Ine ndiri nalo lingaliro labwino.”

Ine ndinati, “Uko nkulondola.”36 Ndipo mmawa wachiwiri. Mosapitirira apo, nditamugwiramnyamatayo padzanja; mmawa wachiwiri, apo panalibengakhale chipsyera pa khutu lakelo. Izo zinali zitapita zonsekwathunthu.37 Nthawi zambiri ife timakanikiza, ndi kuyesera kutitifike ku izi, izo. Kapena…Onani, ndi, “Zizindikiro izizidzamutsatira wokhulupirira.” Iwo sananene kuti “ngati iwoati adzawapempherere odwala.” “Ngati iwo adzaika manjapa odwala, iwo adzachira!” Ife tiyenera tizikhala nachochikhulupiriro, ifeeni, mu zomwe ife tikuchita. Chabwino.38 Kotero tsopano Donavon mwinamwake ali pano. Inumukomana naye iye. Iye akhala ali pano, ngati iye sali panommawa uno, mu zina za zipinda zapamwamba zinazo. Inumukomana naye iye, ndipo iye audziwa umboniwu.39 Ndipo ine ndinganene chiani chinanso? Ine ndikukhulupiriraLuka, kapena Yohane, mmodzi, anati dziko silikanakhozaku-…kugwira, kusunga mabuku omwe akanakhozakulembedwa a zomwe Iye wachita pakati pa anthu mumasiku otsiriza ano; momwe odwala achiritsidwira, zidakhwakuomboledwa, mwa zikwi za iwo, ndi mitundu yonse yamatendandi zosautsa.40 Tsopano, inu uko mu dziko la wailesi, chimodzimodzi kuno,ine ndagwirizira pano tsopano zopempha zambiri zodzazamdzanja zomwe zabwera pa telefoni mmawa uno, imaimbamosalekeza kuyambira pomwe takhala tiri kuno. Ndipo koteroife…Zopempha wani handiredi ndi nainte-sikisi zabwerammawa uno, ndi foni, kuyambira pomwe takhala tiri kuno.Kotero tiyeni ife tilumikizane mu pemphero tsopano pamenealiyense…Kulikonse komwe inu muli, uko mu dziko, ikananimanja pa wina ndi mzake, ngati inu muli okhulupirira. Ngatisichoncho, ikani dzanja lanu pa Baibulo kapena chinachakekunja uko, pamene ife tikupemphera kuno ndi uko.41 Wokondedwa Atate Akumwamba, umboni waung’ono waDonavon Weerts, umodzi chabe pa zikwi, Ambuye, zomwe Inumwachita mwachisomo kwambiri…Ine ndikupemphera kutiInu muyang’ane pansi mu mitima ya anthu konse pano ndimu dziko la wailesi. Ndipo mulole iwo, aliyense, achiritsidwe.Mulole woipayo awasiye iwo, ndipo mulole iwo awomboledwekuchokera ku zosautsa zawo zonse. Perekani izi, Atate. MuDzina la Yesu Khristu, MwanaWanu, ife tikupempha izi. Ameni.“Zikomo Inu, Ambuye.” [Malo osajambulidwa pa tepi—Mkonzi.]

Page 10: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

10 MAWU OLANKHULIDWA

[M’bale Branham akutsiriza kuulutsa kwa wailesiyachiwiri—Mkonzi.]

✩ ✩ ✩ ✩ ✩ ✩ ✩42 Chabwino, izi ndi nthawi zitatu za ine pano mmawauno. Mai! Ndipo, inu mukudziwa, zanenedwa kumene kuti ifetiyenera tichoke mchipinda chino pafupi maminiti khumi ndiawiri, khumi ndi anai, kapena chinachake. Ndipo oyang’aniraanati, ndi ndani ali mu chipinda china icho, ndipo iwo sakhozakupereka zakudya zirizonse. Zakudya zathu zatalikitsidwa. Ifetakhala nako ndi kuperekera kochuluka, inumukudziwa. Koteroife tiri, okondwa kwambiri kuti ife takhala nalo phwandolalikulu, lauzimu, monga ine ndingalitchulire ilo, mmawa unokuno ndi gulu labwino ili la amuna.43 Ine ndikufuna k—kuti nditchule kuti ife tiri…misonkhanokachiwiri, mawa madzulo, uko ku Embassy. Tsopano, ifetidzakhala tikupempherera odwala uko, ndipo tikuyembekezeraMulungu kuti akakomana nafe. Ndipo ine ndabwera kutindidzaikepo gawo langa, utumiki wanga, pa kuupangitsa(zonse zomwe ife tingakhoze) msonkhano uno kuti ukhalewopambana. Osati wopambana chifukwa ndi misonkhanoyathu, koma wopambana kwa anthu pomupeza Yesu Khristu.Ndiko kupambana. Misonkhano iliyonse, ziribe kanthumomwe ife timutamandira Mulungu, ndi zinthu zazikuluzingati zomwe ife tikuziona Iye akuzichita, nthawi zingati Iyeakuyankhula kwa ife mu Mzimu, ndi zina zotero; kupatula ngatipatakhala chinachake chomwe chakwaniritsidwa, miyoyo inaitabweretsedwa mu Ufumu!44 Ndipo M’bale Shakarian tsopano wapanga kumene—nenolenileni posachedwapa la zomwe iye amaganiza za masikuawa omwe ife—ife tiri kukhalamo. Ine ndikukhulupirira moonaizo ndi mtima wanga wonse, kuti ife tikukhala kumene panthawi yotsekera, basi mu—basi mu mithunzi yausiku. Dzuwalapita patsogolo patali. Ndipo pamene ife tikuwona zinthuzikuchitika momwe izo ziriri lero, bwanji, ndi zovuta kunenazomwe kam’badwo kenako kati kabweretse. Masiku pang’onoapitawo…45 Mungondilola ine ndikupatseni inu kamkati kenakakekakang’ono. Iwo anapanga chiwerengero ku Arizona konse,kumene ine ndikukhala, mwa masukulu onse. Iwo anawapatsaana, mwakusadziwa kwa iwo, kuyesa kwa maganizo. Ndipotalingalirani chiani? Kuphatikiza masukulu apamwamba ndi—ndi masukulu a galamala, uko kunali magawo eyite pa zana aana akuvutika ndi kuperewera kwa maganizo. Magawo seventepa zana a iwo anali owonera televizioni. Mwaona, kuipa, izozangozembetsedwera pa ife ndipo ife sititi…Inu mumadabwachifukwa chomwe izo zimabwerera. Inu mukhoza kulimva Liwula Mulungu likukuwa apo motsutsa izo, ndipo apobe kuno ife—ife timadzipeza tokha titakoledwamu izo.

Page 11: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

MMODZI PA MILIONI 11

46 Ndiloleni ine ndikupatseni inu chinachakechonjenjemeretsa. Mwaona, “Si onse omwe anena kwa Ine,‘Ambuye, Ambuye,’ ati adzakalowe umo; koma iwo omweamachita chifuniro cha Atate Anga.” Chifuniro Chake ndi MawuAke. Ife tikhoza kukhala achipembedzo kwambiri kumene,kukhala nazo nthawi zazikulu, kumafuula, kumalumpha, mumisonkhano iyi, chomwe ife tiri…Ine sindiri—ine sindikufunakuti ndikhale wotsutsa. Koma ine ndiri n—nayo ntchito yotindiichitire kwa Mulungu, ndipo ntchito imeneyo ndi kutindikhale wodzipereka ndi kumanena zomwe Iye akufunakuti ine ndizinena. Ndipo ine—ndine woyamikira ndithuchifukwa cha a chaputala chaku California omwe apiriranane mu—mu zondikhudza zanga. Ngati ine sindingayankhulezondikhudza zanga, ndine wachinyengo ndipo tsopano inesindiri nkomwe woonamtima ndi inu. Ndipo ngati inesindingakhale woonamtima ndi inu, ine ndingakhale bwanjiwoonamtima ndi Mulungu, chifukwa ine ndimakuonani inundipo ndimayankhula kwa inu. Ndithudi, ife timateronso, kwaMulungu, ifenso, koma ife tiyenera kuti tizikhala odziperekakwenikweni ndi owonamtima kwa wina ndi mzake. Ifetiri ndithudi mu—woipa, m’badwo woipa. Ndipo kodi inumunayamba mwaimapo…

47 Ndiloleni ine ndikupatseni inu chiwerengero cha pang’onochokha. “Si onse omwe anena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ atiadzalowe; koma iwo omwe achita chifuniro cha Atate Anga.”Yesu ananena, pa dziko lapansi, “Munthu sadzakhala moyo ndimkatewokha, koma ndiMawu onse.”Mawu onse! Osangoti panondi apo, Mawu, koma ndi Mawu onse.

48 Anali Mawu amodzi osakhulupiriridwa, a Mulungu…amalamulo a Mulungu, omwe anayambitsa imfa, chisoni, ndimatenda aliwonse ndi kupweteka kwa mtima, kuphonya Mawua Mulungu, Mawu amodzi! Ngati iye anautengera mtundu waanthu ku imfa, pa kuphonya, kusakhulupirira Mawu amodzi,“ndithudi,” ndithudi. Koma Iye anati izo zikanadzachitika.Satana anati, “Ndithudi izo sizitero.” Koma izo zinatero.

49 Kotero, ife tiyenera kuti tizisunga Mawu aliwonse aMulungu. Ndipo ngati umunthu ndi kuvutika konse uku ndizinthu zomwe zinachitika pa mtundu wa anthu, pa kusokoneza,k—kapena kusawakhulupirira Mawu amodzi, ife tibwererabwanji powaphonya Amodzi, ngati izo zinatengera mtengowonse uwu, ngakhale moyo waMwanaWake?

…ambiri ali oitanidwa,…apang’ono aliosankhidwa.

…ambiri ali oitanidwa,…apang’ono aliosankhidwa.

Page 12: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

12 MAWU OLANKHULIDWA

50 Ine sindingakhoze kutenga nkhani kuchokera apa, komachifukwa ife tiribe nthawi, koma kuti ndingokusiirani inuchinachake. Tiyeni ife tiganizire za…51 Ine ndinapita tsiku lina ndi M’bale Shakarian, komwe iwoanali kupanga haibridi ng’ombe. Ndipo ine ndinawona—a…mu laboratore momwe M’bale Shakarian ananditengeramo ine.Ndipo iwo anamiza mu umuna wa ng’ombe yaimuna, pang’onopokha…konga ka chida kakang’ono, ka mtengo wa machesi,ndipo anatungamo gulu la umuna umenewo, ndipo anawuikaiwo pansi pa galasi ili lomwe linazikulitsa izo nthawi mazana.Ndipo apo panali nyongolosi zazing’ono zikulumpha umo, muumuna uwo. Chimene, ife tikudziwa nyongolosi zimabwerakuchokera kwa yamphongo, ndipo dzira limachokera kwayaikazi. Ndipo ine ndinamufunsa wa zamankhwala apo,ine ndinati, “Ndi chiani chomwe chikupangitsa kulumphakwakung’ono uko monga choncho?”

Iye anati, “N—ndito ting’ombe tamphongo ndi tathazi.”Mwaona?

Ndipo ine ndinati, “Mu dontho laling’ono ilo?”

Iye anati, “Eya.”52 Ine ndinati, “Mwinamwake ndiye mu umuna wonsewomungakhale muli mamilioni a iwo?”

Iye anati, “O, eya.”Mwaona?Ndipo ine ndinayang’anitsitsa.53 Tsopano, pamene chinthu chopambana ichi chimafikapochitika, pamakhala dzira limodzi likuyembekezera nyongolosiimodzi kuchokera mu milioni iyo. Ndipo palibe mmodziyemwe angadziwe kuti nyongolosi imeneyo ndi iti, kapena ndidzira liti lomwe ilo liri. Ngati inu mungayang’ane kubadwakwa chilengedwe, ndi chinsinsi mochuluka kuposa—kuposakubadwa kuchokera kwa namwali. Chifukwa, mu umuna uwu,pamakhala mmodzi mkati umo yemwe anakonzedweratu kutiakhale moyo, ndipo ena onse awo adzafa. Ndipo si woyambakukomanawo ayi; ndi woyamba kubwera palimodzi ndi dziralo.Mwina dziralo likhoza kutulukira kumbuyo kwa umuna, kapenapakati pa umuna; nyongolosi ikhoza kuchita chimodzimodzi,dzira. Nyongolosi imakwawira kukalowa mu dziralo, ndipotimichira tating’ono timathothoka pa ito, ndipo pamenepopamayamba nsana. Pamakhala imodzi yokha mu gulu lonse ilo,la milioni, yomwe iti ikwaniritse izo, imodzi yokha; ndipo izozimapangitsidwa ndi Mphamvu ina yosadziwika, kwa munthu.Komabe ndinu, aliyense, ofanana, iliyonse ya nyongolosizimenezo ndi zofanana basi. Chinthu chomwecho mwa zinyama.Chinthu chomwecho mwa munthu. Iyo imapangitsidwa ngatiuyo ati adzakhale mnyamata, msungwana, wa mutu-wofiira,wa mutu-wakuda, kapena chiani. Izo zimapangitsidwa ndiMulungu. Zonse izo zimawoneka zofanana, mwachilengedwe,

Page 13: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

MMODZI PA MILIONI 13

koma pamakhala mmodzi mmenemo yemwe amadzozedwera kumoyo;mmodzi pamilioni, komabe zina zonse za izo nzofanana.54 Pamene Israeli ankachoka ku Igupto, iwo analipo pafupifupianthu thuu milioni anachoka pa nthawi yomweyo. Aliyensewa iwo anaumva uthenga wa mneneri. Aliyense wa iwoanaliwona Lawi la Moto. Aliyense wa iwo anabatizidwira kwaMose, mu Nyanja Yofiira. Aliyense wa iwo anafuula m—muMzimu, anaimba nkhotcho ndi kumathamanga chokwera ndichotsika nalo gombelo, ndi Miriamu, pamene Mose ankaimbamu Mzimu. Iwo, aliyense, anamwa kuchokera mu Thanthwelauzimu lomwelo. Iwo, aliyense, ankadya Manna atsopano usikuuliwonse. Aliyense wa iwo! Koma panali awiri anakafika kudzikolo, mmodzi pa milioni.55 Kodi yeserolo linali chiani? Iwo onse ankamwamuThanthwelomwelo, iwo onse ankadya Manna auzimu omwewo momwe ifetikudyerammawa uno, koma kuyesa kwaMawu kunatsimikiziraizo. Pamene izo zinafika ku nthawi ya Kadeshi-barnea,pamene iwo anauyamba waku dziko lolonjezedwa, ndipo iwosakanakhoza kupitako mpaka iwo atayesedwa ndi Mawu. Ndipoonse—khumi enawo anabwerera, ndipo anati, “Ife sitingakhozekulitenga ilo! Anthuwo ali ngati…Ife tiri ngati ziwala, kwaiwo, mzinda wao waukulu wa mu mpanda. Kutsutsako ndikwakukulu kwambiri.”56 Koma Yoswa ndi Kalebu anawatontholetsa anthuwo. Iwoanati, “Ndife oposa agonjetsi kuti tichite izo!” Chifukwa?Mulungu anati, iwo asanachoke ku dziko lolonjezedwalo, “Inendakupatsani inu dzikoli. Ine ndalipereka ilo kwa inu. Ndi lanu.”Koma apo panali mmodzi pa milioni iliyonse.57 Alipo pafupifupi mamilioni mazana asanu otchedwaAkhristu mu dziko lero, ndipo tsiku lirilonse limathetsa kam’badwo. Ndipo tsopano, bwanji ngati Mkwatulo ukanatiubwere lero ndipo anthu faifi handiredi, konsekonse, akanatiatengedwere mu Mkwatulo? Inu simukanati mudziwe nkomwekapena kuziwona mu pepala, zakuti iwo apita. Ndipo Kudzakwa Ambuye ndi Kudza kwachinsinsi. Iye adzabwera ndikudzawabapo. Iwo adzakhalapo apang’ono chotero,mpaka…58 Basi monga momwe izo zinaliri mu masiku pameneophunzira anamufunsa Yesu, “Nchifukwa chiani Alembiamanena kuti—kuti Eliya ayenera kudza poyamba?”

Iye anati, “Iye anadza kale, ndipo inu simunazidziwenkomwe izo.”59 Kodi inu munayamba mwaganizapo zomwe anthuwoanachita? Iwo anapita akukhulupirirabe kuti Mo-…kuti Eliyaanali nkudza. Ndipo iye anali pakati pawo pomwe, ndipo iwosankazidziwa izo.60 Chomwecho izo zidzakhala ziri mu Kudza kwa Mwanawa munthu! Iwo adzachita naye Iye chinthu chomwecho basi.

Page 14: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

14 MAWU OLANKHULIDWA

Mzimu wa Mulungu uli pano. Chabwino, kodi ife tichita nawochiani Iwo? Kodi ife tizidya Manna, ndi zina zotero, ndipoosamasunthirammwambamopitirira pamene ife tikukula?

61 Kodi inu munayamba mwazindikirapo mbewu, mongaM’busa Pitts anali kuyankhula mphindi zingapo zapitazo, ndimomwe mbewu imapitira mu nthaka? Mumakhala mbewuzambiri mu nthaka umo. Pamene Mulungu anasunthira pamadzi, ndi Kuwala, ndipo Kuwala kunatulukirapo. Kukhalapokoyamba kwa Mulungu, Kuwala koyankhulidwa kunadza ndiMawu a Mulungu. Ndipo Mawu a Mulungu ndi chinthu chokhachomwe chiri kubweretsabe Kuwala. Ndipo pamene madzianapita mmbuyo, mbewu zinali kale ziri mu nthaka, ndipoKuwala kunangobweretsapo mbewu zomwe zinatsalira ndinyongolosi mkati mwa izo, zinatulukirapo. Mulungu akupangachirengedwe Chake.

62 Ndipo tsopano, pa mmawa wa Isitara apo panali Kuwalakwina komwe kunakhudza dziko lapansi, pamene MzimuWoyera unaperekedwa.Ndipo Iwo unaperekedwa kuti ubweretseKuwala kwa Mbewu izo zomwe Mulungu, mwa kudziwiratuKwake, anazidziwa kuti zikanadzakhala ziri pano pa dzikolapansi. Monga Iye anadziwira mbewu yoyamba yachilengedwe,Iye amadziwa komwe Mbewu yauzimu ili. Thupi lanu linali liripano pomwe pa dziko lapansili, pamene Mulungu analibweretsakoyamba dziko lapansi mu kukhalapo. Ife ndife gawo la dzikolapansi. Ife tinali mkati mmenemo. Ndipo mwa kudziwiratuKwake Iye ankadziwa ndendende yemwe akanati adzamukondeIye ndi yemwe akanati adzamutumikire Iye, ndi yemwesakanadzatero. Kudziwiratu Kwake kumanena zimenezo. Ngatiiko sikutero, ndiye Iye si Mulungu. Iye sangakhoze kukhalaMulungu popanda kukhala wopandamalire. Ndipo ngati Iye aliwopandamalire, Iye amadziwa zinthu zonse.

63 Kotero, inu mumawaona anthu akupanga kulakwitsakwawo. Iwo amapunthwa pa izo. Iwo amathamanga pamwambapa izo, ndipo iwo amaganiza ichi ndi icho, koma izo sizimagwirantchito bwino, ife timaziwona izo. Koma pali kugwira ntchitokwabwino, ndiko kupeza chifuniro changwiro cha Mulungu ndikuimamu icho, chomweMulungu anakuitanirani inu.

64 Monga M’bale Jack ananena mphindi zingapo zapitazo zakumusi kuno ku—Pershing Square, chisokonezeko chonse. Winambali iyi, ndi wina mbali iyo; ndi za azafioroje, ndi zina zotero,kuti inu ngati mukufuna kuti mudziwe za fioroje, pitani kumusikumeneko.

65 Ine ndikulingalira kuti izo ziri basi monga ziri ku Hyde Parkmu London. Ine ndinali kumeneko, aliyense anali ndi lingalirolake lake. N—ndi chisokonezeko cha tsiku la dziko lamakono muBabeloni.

Page 15: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

MMODZI PA MILIONI 15

66 Koma kodi inu munazindikira monga—monga M’bale Pittsanapitirira ndi uthenga wake wokondedwa mmawa uno kwaife? Pamene iye anayamba kuyenda kuchoka mu parkiyo,pamenepo iye anapeza kakombo wamng’ono wa Isitara. “Pakatipa chisokonezeko chonsecho,” momwe iye anazibweretsera izokwa ife, “iye analibe njira yonenera ‘inde’ kapena ‘ayi.’ Iwo unalimoyo waMulungu ukuwalamkati umo, pakati pa chisokonezekochonsecho.” Iwo unali apo mwa kuwala kwake, chifukwaMulungu anali atazidzoza izo kuti zidzakhale pamenepo. Pakatipa mkangano wonse, panalibe wina yemwe ankazindikira iwo.Iwo sankawonamachitidwe auzimu akewo.67 Ndipo mmomwe izo ziri lero pakati pa kusonkhana kwathukonse kwakukulu ndi magulu, ndi mipingo ndi zipembedzo, ndizina zotero. Wina akukokera mbali iyi, “Ife tiyenera tikhaleAchibaptisti, kapena tikhale Achipresbateria, tiyenera tikhaleichi, icho, kapena chinacho.” Pakati pa izi zonse, pali duwalomwe likumela. Ilipo mphamvu ya Mulungu pakati pathupomwe, ikukulitsidwa pakati pa ife tonse. Tiyeni tingoimandipo tiiwone iyo, maminiti pang’ono, ndipo tiiwone iyo Sabataino, ndipo tiiwone iyo ikufutukuka patsogolo pathu pomwe.Ife tikukhulupirira kuti Mulungu achita izo. Sichoncho inu?[Osonkhana ati, “Ameni.”—Mkonzi.]68 Ine ndikuwona kuti ife timayenera kukhala mu zipindazapansi pano. Kotero tiyeni tipemphere, aliyensewa ife.69 Wokondedwa Mulungu, pamene ife tikuweramitsamitu yathu mu Kukhalapo Kwanu, ife tikumverera kutindife osakwanira kwambiri kuti tikupempheni inu. KomaInu munatilonjeza ife kuti, ngati ife titi tibwere, Inusimukanati mutikanize ife. Ndipo maneno amwano awa omweangopangidwa kumene, mwanjira iliyonse sikuti chikhalechiphunzitso, “mmodzi pa milioni,” koma basi kuti tizikhalangati tikukumbukira. Pakuti Inu munati:

…khwalala ndilo chipata, ndipo njirayo ndiyopapatiza, yomwe ikulondolera ku moyo, ndipoadzakhalapo ochepa omwe ati adzaipeze iyo.Pakuti ambiri ali oitanidwa, koma apang’ono ali

osankhidwa.70 O Atate Amuyaya, tumizani Kuwala kwa Uthenga kudutsamu mzinda uno, kudutsa mu sabata ikudza iyi ya msonkhanowaukulu. Ndipo ngati pangakhale pali Mbewu iliyonse,mwanjira ina mwa kupereka Kwanu Komwe kwakukulu,kwanzeru, monga ndayesera kuzilongosola izo mu umunawa champhongo ndi chachikazi, mulole izo zifike mpakamu msonkhano waukulu. Mulole Mzimu Woyera uwapatseiwo Kuwala. Ife tikuzindikira kuti nthawi mwinamwake ilimochedwa kuposa momwe ife tikuganizira kuti iyo ili. Ifetikupemphera, Mulungu, kuti pamene ife tikubwera kuno,

Page 16: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

16 MAWU OLANKHULIDWA

tikungokhulupirira kuti mwinamwake pali chinachake panochomwe chingakhoze kuchitidwa chomwe chingawathandizeanthu, kapena—kapena kuigwira nkhosa yotsiriza iyo. Ifetikudziwa, pamene khola lidzadzaza, ndiye M’busa adzatsekachitseko.71 Momwe izo zinaliri monga mu masiku a Nowa, pamenemembala wotsiriza wa banjalo anabweretsedwa mkatimo,Mulungu anatseka chitseko. Ndipo iwo anamenya ndi kuguguda,koma izo zinali mochedwa kwambiri. Wokondedwa Mulungu,iwo anali nawo mwayi.

Inu munati, “Ine ndine Khomo limenelo la ku khola lankhosa.”72 Ndipo kukhudza kwake nyimbo yochokera kwawandakatulo, “Kodi nainte naini si zokwanira kwa Inu? Koma,ayi, inalipo imodzi ina.” Iyo ikhoza kukhala nkhosa yaing’onoyakuda, kapena iye akhoza kukhala winawake wopanda pake,akhoza kukhala wamng’ono wamkazi kapena wamwamuna.Ife sitikudziwa komwe iwo ali, koma mmodzi wotsirizayoayenera kuti abweremo ndiyeno chitseko chidzatsekedwa. OMulungu, Yemwe mumadziwa zinthu zonse, ifufuzeni mitimayathu mmawa uno. Ndipo mutitumize ife kulikonse komwe ifetingakhoze kupitako, kuti ife tikakhoze kukamupeza wotsirizauyo, kuti chitseko chidzatsekedwe ndipoM’busa akhale alimkatindi nkhosa. Perekani izi, Ambuye. Ngati alipo mmodzi uyo panolero, ngatimmodzi uyo yemwe akuyenera kuti abweremo…73 “Onse omwe Atate andipatsa Ine adzadza kwa Ine.Ndipo palibe munthu angakhoze kudza, kupatula Atate Angaatamukoka iye.”74 Ndipo ngati pali kukoka, kapena kumverera kwakung’ono,kuti ili likhoza kukhala ora la winawake pano mwa omvetseraawa, muno kapena mzipinda zapansi, kapena kulikonse komweiwo angakhale ali, mulole iwo ayankhe, “Inde, Ambuye, ndinewamng’ono wolowererayo yemwe walowerera kutali; ndiyemwe waumenyera Iwo kumbali, moyo wanga wonse. I—i—ine ndimamverera kuti ine ndikanati ndibwere, koma leroine ndikukakamira ku mbali ya kugonja. Ine sindingakhozekukwera mmwamba kapena kutsika. Ine sindingapitekulikonse.” O, mulole M’busa wamkulu adze, afikire pansi ndimanja ofewa ndipo amubweretse mmodzi uyomotetezekamkati,amuike iye pa mapewa Ake ndi kumubweretsa iye abwereremotetezeka.75 Mwinamwake alipo mmodzi pano, Ambuye, yemweakudwala, mu chikhalidwe chomwecho, chomwe adotolo anati,“Palibe chomwe chingakhoze kuchitidwa.” Iyewayesera zolimbakuti awapulumutse iwo, koma iye sakanakhoza kuwupulumutsaiwo. Icho chiri patali kwa kufikira kwake. Pali—palibe kanthukomwe iye angakhoze kuchita. Mankhwala ake kapena mpeni

Page 17: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

MMODZI PA MILIONI 17

wake sukanakhoza kufikira kwa icho. Koma, O Ambuye,palibe chinthu chomwe chiri kutali kwambiri kwa nkonoWanu waukulu, ndipo Mawu Anu ndiwo nkono Wanu. Koteroife tikupemphera, Wokondedwa Mulungu, kuti, mmawa uno,pamene ife tikuyankhula kwa Inu, kuti inu mufikira pansindipo mumutenga uyo yemwe akudwala ndipo sangakhozekudzithandiza yekha, kutali ndi kufikira kwa zinthu zonseza mwasayansi, kutali ndi adotolo, mulole iwo achiritsidwe.Perekani izi, Ambuye.76 Pamene ife tikuganizira za Davide, pamene iye anapatsidwaulamuliro pa nkhosa zapang’ono, zapang’ono chabe. Koma tsikulina chimbalangondo chinabwera umo ndipo chinadzagwirankhosa imodzi yaing’ono ija ndipo anaitengera iyo kunja,ndipo chikanaidya iyo (monga khansara ikhoza kudyerathupi), kapena mkango waukulu. Koma Davide, posakhalandi zida mwabwino—ndi mfuti, kapena, posakhala mwamunawalupanga, koma ndi kalegeni kokha, iye anapita motsatirankhosa imeneyo. Ndipo pamene iye anaipeza—chinyamachomwe chinali pafupi kuti chiiphe nkhosa yaing’onoyo,iye anachipha icho ndi kugenda kwa legeni. Basi kachidakakang’ono ndi chidutswa cha chikopa ndi chingwe, ndipo,koma iye anali ndi chidaliro mwa izo.77 Ife tiribe namatetulewamkulu pakati pathu, Ambuye. Ife ndianthu ophweka tiri ndi pemphero laling’ono lophweka, komaife tikubwera mmawa uno kutsatira nkhosa ya Atate. Mkaziuyo yemwe wayenda mmisewu, momvetsa chisoni, akusutandudu, akuyesera kuti apeze mtendere kupyolera mu ndudu;mwamuna yemwe wanunkhiza galasi ndipo wayesera kumaliikailo mmbuyo, koma mdani akumugwira iye zolimba; mnyamatauyo kapena msungwana yemwe wayesera kuti achite molondola,yemwe sakukhoza basi kupeza nyonga zoti achoke ku chinthucholakwikacho; ife tikubwera mu Dzina la Ambuye Yesu,kuti tidzaitenge nkhosa imeneyo mmawa uno. Ife tikumunyozamdani; chifukwa ndi chinthu chophweka, kugenda kwa legeni,pemphero, koma ife tikubwera kuti tidzamubwezere ameneyoku khola la Atate, kuti ife tikhoze kupereka chiwerengerocha zinthu izo zomwe zaperekedwa mu dzanja lathu. Mulolemphamvu ya Mulungu tsopano ikhudze chikhulupiriro, pansimu mitima ya anthu, ndipo mulole moyo wotaika uwo ubwereremmawa uno. Mulole mayesero a moyo uno awamasule iwoachokepo, amulole iye azipita. Ndipo mulole iye adzipeze aliwotetezeka pa mapewa a Mbuye, atanyamulidwa kubwereraku chitetezero kachiwiri. Ife tikupempha izi mu Dzina laYesu. Ameni.78 Mulungu akudalitseni inu nonse. Mpaka ine ndidzakuoneniinu mawa, ine ndikubwezera msonkhanowu kwa M’baleShakarian. [Malo opanda kanthu pa tepi—Mkonzi.]

[M’bale Branhamakutsirizitsa gawo la chitatu—Mkonzi.]

Page 18: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

18 MAWU OLANKHULIDWA

✩ ✩ ✩ ✩ ✩ ✩ ✩79 Ichi, i—ine ndikuyembekeza kuti inu mu…kuti ine ndipezachisomo chochuluka pamaso pa Mulungu ndi pamaso painu, kuti mukhulupirira kuti ine ndikhoza kuima pano kutindizikuuzani inu chinachake chomwe chinali cholakwika. Inendinadutsa tsiku la kubadwa kwanga la fifite-sikisi, tsikulina lija. Uwu si Uthenga wa bambo wokalamba chabe. Inendazikhulupirira izi kuyambira pomwe ine ndinali mnyamatawamng’ono. Ndipo ngati izi si zoona, ine ndakhala ndiri munthuwopusa kwambiri yemwe Mulungu anayamba wakhalapo nayepa dziko lapansi. Ine ndauperekamoyowangawonse pa cholingaIchi. Ndipo mundilole ine ndinene izi ndi kudzipereka: ngatiine ndikanakhala ndi miyoyo zikwi khumi, ine sindikanasinthakonse lingaliro langa.80 Tsopano, machiritso ndi ofikirika ndi munthu aliyese.Kumbukirani, machiritso ali mwa inu. Mulungu anaika mumtengo wa pichesi pichesi aliyense yemwe akanati adzakhalepokonse mmenemo, pamene Iye ankamubzala iye mMunda.Mwaona, inu basi…mtengo wa pichesi kapena mtengowa apulo, kapena mtengo wa chipatso, umangoyenera kutiuzikula, kuchokera pakumwa madzi mu nthaka. Tsopanoaliyense wa inu ali nazo zokhozetsa zimenezo mwa inu, kutizikupulumutseni inu, pakuti izo ndi Mulungu, kuyambirapamene inu munabzalidwa mwa Khristu mwa ubatizo (osatiubatizo wa madzi), ubatizo wauzimu. Inu simumabwera mwaKhristu ndi ubatizo wamadzi. Mwa ubatizo wauzimu!81 Mawa madzulo, Ambuye akalola, ine ndidzayankhula pazimenezo,momwe ndi chomwe chiri kachititsidwe kake kenikenika Iwo. Ife tidzakhala nazo izo madzulo kotero kuti izosizidzasokonezana ndi iliyonse yamisonkhano yanu.82 Tsopano taonani, aliyense wa inu pano akuima ngatiokhulupirira, onani, ndiye Moyo umene unali mwa Khristu ulimwa inu. Iwo ukhoza, ngati inumutati mungoziwona izi!83 Ndi ntchito ya Mdierekezi kuti azikusiyani inu muliotchingidwa kwa Izo, kukuchititsani inu khungu. Iyeamangokusiyani inu mukhale akhungu, ndizo, onani, inusimumadziwa komwe inu mukupita ndiye. Munthu yemweali wakhungu sangakhoze kudziwa komwe iye akupita, iyeamayenera kuti afunefune kumvetsa kuchokera kwa winawakeyemwe angakhoze kuwona. Mpaka ife titakhoza kumvetsa,winawake akuyenera kuti atiuze ife chomwe chiri Choonadi.84 Ndipo Khristu anakuferani inu, ndipo inu mwawokeredwakuchokera ku dziko mwa Khristu. Ndipo chirichonse chomweinu mukuchisowa chiri mwa inu momwemo, mwa ubatizo waMzimu Woyera. Si kulondola uko? Tsopano chinthu chokhachomwe inu mukuyenera kuti muzichita ndicho kungoyambakumamwa kuchokera kwa Iwo.

Page 19: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

MMODZI PA MILIONI 19

85 Ndipo pamene mtengo uli kumwa, iwo umayambakukankhira kunja masamba ake, timphukira take, umakankhirakunja chipatso chake chaka chirichonse. Chipatsocho sichiri munthaka; chipatso chiri mu mbewu. Ndi angati akumvetsa izo,nenani “ameni.” [Osonkhana ati, “Ameni.”—Mkonzi.] Kotero,mwaona, chipatso chiri mu mbewu, ndipo mbewu iliyonseimayenera kuti izimwa kuchokera ku kasupe wake. Pamenemvula ivumba, imaipatsambewu imeneyo, moyo, kuti izimwako.Ndipo, pamene iyo ikumwa, iyo imakula.86 Ndipo iyo imakula mpaka iyo imafika ku kuphukakwathunthu, chimodzimodzi monga momwe Mpingo wachitira,kuyanga mu m’badwo uno.87 Ndipo, pamene ife tikumwa, ife timakula. Koma ngatimbewuyo ikana kumwa, ndiye mbewuyo siingakhoze kukula.Ndipo ngati inumutimungokhulupirira izo tsopano, payekha!88 Chifukwa, inu mukudziwa momwe Ambuye amachitira,amasonyeza zinthu zosiyana, za zomwe inu mwazichitandi zomwe simukanayenera kuzichita, ndi zina zotero, mumsonkhano. Ife timayembekeza kuti MzimuWoyera ukanagwerapa ife mmawawu ndi kuchita zoterozo, pamene ife tinaimira.Koma ine ndinapitirira kuyembekezera.89 Ine ndikuganiza ndi gawo lamanjenje, poganizira kutizipinda zapansi amafuna kuti ife titulukemo muno, mwaona.Koma iwo akutifuna ife; ife tachedwa tsopano.90 Koma khulupirirani izi, ndi mtima wanu wonse. Chondeteroni. Ngati i—ngati ine ndapeza chisomo pamaso panu, ngatimunthu woona, khulupirirani izi. Tsopano ikani manja anu pa—pa wina ndi mzake.91 Tsopano penyani, tsopano, Baibulo silinati, “Zizindikiro izizidzamutsatira William Branham.” Silinati, “Izo zidzamutsatiraOral Roberts yekha.” Silinati, “Izo zidzamutsatiraM’baleKopp,”kapena winawake.92 “Zizindikiro izi zidzawatsatira iwo,” ambiri, “omweakhulupirira. Ngati iwo aika manja awo pa odwala, iwoadzachira.” Ndi Mphamvu ya Mulungu yomwe ili mwa inu,yomwe imaubweretsa Moyowo kwa munthu yemwe inumwaikapo dzanja lanu, gwero loperekera Moyo la MzimuWoyera.93 Wokondedwa Mulungu, mu Dzina la Yesu Khristu, mumphindi yovuta ino pamene mpingo…mulole iwo aimekachiwiri aka, mopanda manjenje, ndipo mulole Mphamvuyomwe inamuukitsa Khristu kuchokera kumanda, ifulumizitsirekwa iwo pakali pano Choonadi cha Uthenga, kuti kutuma kwaYesu kunali, ngati iwo “aika manja pa odwala, iwo adzachira.”Mulole mphamvu ya chiwanda iliyonse, matenda aliwonse,nthenda iliyonse, kusautsika kulikonse, chinthu chozunzachirichonse chomwe chachitika kwa anthu, mulole zithawe

Page 20: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

20 MAWU OLANKHULIDWA

pakali pano mwa chikhulupiriro. Monga anthu okhulupirira, ifetikupempha izi muDzina la YesuKhristu. Ameni.94 Tsopano kwezani manja anu ndipo zimupatsani Iyematamando, ngati inumukukhulupirira kuti Iye akuchita izo.95 Wokondedwa Mulungu, mwana uyu afa, Ambuye, kupatulaizi zitachitidwa. Ine ndikutsutsa mfundo iyi, mu Dzina la YesuKhristu.Mulole zimusiyemwanawosalakwayu. Ameni.

Tsopano, madotolo ayesera izo, ndipo iwo alephera.Ingokhulupirirani.

Page 21: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

MMODZI PA MILIONI CHA65-0424(One In A Million)

Uthenga uwu wa M’bale William Marrion Branham, woperekedwa muChingerezi Loweluka m’mawa, Epulo 24, 1965, pa kadzutsa wa a Full GospelBusiness Men’s Fellowship International ku Clifton’s Cafeteria mu Los Angeles,California, U.S.A., unatengedwa kuchokera pamatepi ojambulidwa ndi maginitonudindidwa mosachotsera mawu ena mu Chingerezi. Kumasulira kwa Chichewauku kunadindidwa ndi kugawidwa ndi Voice Of God Recordings.

CHICHEWA

©2014 VGR, ALL RIGHTS RESERVED

VOICE OF GOD RECORDINGS, MALAWI OFFICE

P.O. BOX 51453, LIMBE, MALAWI

VOICE OF GOD RECORDINGS

P.O. BOX 950, JEFFERSONVILLE, INDIANA 47131 U.S.A.www.branham.org

Page 22: CHA65-0424 Mmodzi Pa Milioni VGR - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA65-0424 One In A Million VGR.pdf · yochitira izo. N—nthawi ndi ora lomwe ife tiri kukhalamo,

Chidziwitso kwa ofuna kusindikiza

Maufulu onse ndi osungidwa. Bukhu ili mukhoza ku printa kunyumba kwanu ngati mutafuna kuti mugwiritse ntchito inuyo kapena kuti mukawapatse ena, ulere, ngati chida chofalitsira Uthenga wa Yesu Khristu. Bukhu ili simungathe kuligulitsa, kulichulukitsa kuti akhalepo ambiri, kuikidwa pa intaneti, kukaliika pakuti ena azitengapo, kumasuliridwa mu zinenero zina, kapena kugwiritsidwa ntchito ngati njira yopezera ndalama popanda chilolezo chochita kulembedwa ndi a Voice Of God Recordings®.

Ngati mukufuna kuti mumve zambiri kapena ngati mukufuna zipangizo zina zimene tiri nazo, chonde mulembere ku:

Voice of God RecoRdinGsP.o. Box 950, JeffeRsonVille, indiana 47131 U.s.a.

www.branham.org